Numeri 18 BL92

Udindo wa ansembe ndi Alevi, ndi zolandira zao

1 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya nchito yanu ya nsembe.

2 Ndiponso abale ako, pfuko la Alevi, pfuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la cihema ca mboni.

3 Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa cihema conse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.

4 Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa cihema cokomanako, kucita nchito yonse ya cihema; koma mlendo asayandikize inu.

5 Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israyeli.

6 Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kucita nchito ya cihema cokomanako.

7 Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe mucite nchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsaru yocinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani nchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

8 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israyeli; cifukwa ca kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.

9 Izi ndi zako pa zinthu zopatulikitsa, zosafika kumoto; zopereka: zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zaucimo, ndi nsembe zao zonse zoparamula, zimene Andibwezera Ine, zikhale zopatulikitsa za iwe ndi za ana ako amuna.

10 Muzizidya izi monga zopatulikitsa; mwamuna yense adyeko; uziyese zopatulika.

11 Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israyeli; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko.

12 Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa, zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.

13 Zipatso zoyamba zonse ziri m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.

14 Ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zako.

15 Ziri zonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.

16 Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za rowezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndarama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.

17 Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwace mwazi wace pa guwa la nserobe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya pfungo lokoma kwa Yehova.

18 Ndipo nyama yace ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.

19 Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamcere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.

20 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe colowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi colowa cako pakati pa ana a Israyeli.

Limodzi la magawo khumi ndilo gawo la ansembe

21 Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israyeli, likhale colowa cao, mphotho ya pa nchito yao alikuicita, nchito ya cihema cokomanako.

22 Ndipo kuyambira tsopano ana a Israyeli asayandikize cihema cokomanako, angamasenze ucimo kuti angafe.

23 Koma Alevi azicita nchito ya cihema cokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale naco colowa pakati pa ana a Israyeli.

24 Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israyeli, limene apereka nsembe, yokweza kwa Yehova, likhale colowa cao; cifukwa cace ndanena nao, Asadzakhale naco colowa mwa ana a Israyeli.

25 Ndipo Yehova ananena ndil Mose, nati,

26 Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israyeli, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale colowa canu cocokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.

27 Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala.

28 Momweno inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yocokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israyeli; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.

29 Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zace.

30 Cifukwa cace unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zace, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa,

31 Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa nchito yanu m'cihema cokomanako.

32 Ndipo simudzasenzapo ucimo, mutakwezako zokometsetsa zace; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israyeli, kuti mungafe.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36