Numeri 35 BL92

Midzi ya Alevi

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Moabu, pa Yordano, ku Yeriko, ndi kuti,

2 Uza ana a Israyeli, kuti apatseko Alevi colowa cao cao, midzi yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira midzi.

3 Ndipo midzi ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.

4 Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono cikwi cimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.

5 Ndipo muyese kunja kwa mudzi, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwela mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mudziwo pakati; ndiwo mabusa a kumidzi.

6 Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyd midzi ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzace athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.

7 Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo midzi makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.

8 Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yao yao ya ana a Israyeli, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa colowa cao adacilandira.

Midzi yopulumukirako

9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10 Nenandi ana a Israyeli, nuti nao, Pakuoloka inu Yordano kulowa m'dziko la Kanani,

11 muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzace wosati dala athawireko.

12 Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzace asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.

13 Ndipo midziyo muipereke ikukhalireni midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako.

14 Mupereke midzi itatu tsidya lino la Yordano, ndi midzi itatu mupereke m'dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.

15 Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti ali yense adamupha munthu osati dala athawireko.

16 Koma akamkantha ndi cipangizo cacitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

17 Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

18 Kapena akamkantha m'dzanja muli cipangizo camtengo, cakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

19 Wolipsa mwazi mwini wace aphe wakupha munthuyo; pakumkumika amuphe,

20 Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;

21 kapena kumpanda ndi dzanja lace momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo pomkumika.

22 Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamialira,

23 kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wace, kapena womfunira coipa;

24 pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzaceyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;

25 ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere ku mudzi wace wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.

26 Koma wakupha munthu akaturuka nthawi iri yonse kulumpha malire a mudzi wace wopulumukirako kumene anathawirako;

27 nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mudzi wace wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kucimwira mwazi;

28 popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wace wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lace lace.

29 Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la ciweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.

30 Ali yense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.

31 Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, naparamula imfa; koma aziphedwa ndithu.

32 Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira ku mudzi wace wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa wansembe.

33 Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko cifukwa ca mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.

34 Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pace; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36