Numeri 16 BL92

Kora, Datani, ndi Abiramu aukira Mose

1 Koma Kora, mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

2 ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna: mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israyeli, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

3 Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?

4 Pamene Mose anamva ici anagwa nkhope yace pansi;

5 nanena ndi Kora ndi khamu lace lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ace ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa iye.

6 Citani ici; dzitengereni mbale za zofukiza, Kora, ndi khamu lace lonse;

7 nimuikemo moto, muikenso cofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.

8 Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi;

9 kodi muciyesa cinthu cacing'ono, kuti Mulungu wa Israyeli anakusiyanitsani ku khamu la Israyeli, kukusendezani pafupi pa iye, kucita nchito ya kacisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

10 ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? ndipo kodi mufunanso nchito ya nsembe?

11 Cifukwa cace, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye?

12 Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako:

13 kodi ndi cinthu cacing'ono kuti watikweza kuticotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kutipha m'cipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

14 Ndiponso sunatilowetsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kapena kutipatsa colowa ca minda, ndi minda yamphesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao? Sitifikako.

15 Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira copereka cao; siodinalanda buru wao mmodzi, kapena kucitira coipa mmodzi wa iwowa.

16 Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;

17 nimutenge munthu yense mbale yace yofukizamo, nimuike cofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yace yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yace yofukizamo.

18 Potero munthu yense anatenga mbale yace yofukizamo, naikamo moto, naikapo cofukiza, naima pa khomo la cihema cokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

19 Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la cihema cokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.

Alangidwa oukirawo

20 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

21 Dzipatu, leni pakati pa khamu lino, kuti ndi wathe m'kamphindi.

22 Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24 Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kucoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.

25 Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akuru a Israyeli anamtsata.

26 Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Cokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kali konse, mungaonongeke m'zocimwa zao zonse.

27 Potero anakwera kucokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anaturuka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna, ndi makanda ao.

28 Ndipo Mose anati, Ndi ici mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kucita nchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwanga mwanga.

29 Akafa anthu awa monga amafa anthu onse, kapena akasungika monga amasungika anthu onse, Yehova sananditumiza ine.

30 Koma Yehova akalenga cinthu catsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pace, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.

31 Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang'ambika pansi pao;

32 ndi dziko linayasama pakamwa pace ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.

33 Comweco iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.

34 Ndipo Aisrayeli onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kupfuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.

35 Ndipo mota unaturuka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera naco cofukiza.

Alanditsa mbale zofukiza za oukirawo

36 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

37 Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali; pakuti ziri zopatulika;

38 mbale zofukizazo za iwo amene adacimwira moyo wao wao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale cibvundikilo ca guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, cifukwa cace zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala cizindikilo kwa ana a Israyeli.

39 Ndipo Eleazara wansembe anatenga mbale zofukiza zamkuwa, zimene anthu opsererawo adabwera nazo; ndipo anazisula zaphanthiphanthi zikhale cibvundikilo ca guwala nsembe;

40 cikhale cikumbutso kwa ana a Israyeli, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kucita cofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lace; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.

Anthu adandaula, mliri uwaononga

41 Koma m'mawa mwace khamu lonse la ana a Israyeli anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.

42 Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anaceukira cihema cokomanako; taonani, mtambo unaciphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.

43 Ndipo Mose ndi Aroni anadza kukhomo kwa cihema cokomanako.

44 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

45 Kwerani kucoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi.

46 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo mota wa ku guwa la nsembe, nuikepo cofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwacitire cowatetezera; pakuti waturuka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.

47 Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo cofukiza nawacitira anthu cowatetezera.

48 Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka.

49 Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera cija ca Kora.

50 Ndipo Aroni anabwera kwa Mose ku khomo la cihema cokomanako; ndi mliri unaleka.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36