Numeri 29 BL92

1 Ndipo mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.

2 Pamenepo muzipereka nsembeyopsereza ya pfungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi opanda cirema;

3 ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,

4 ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

5 ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo, yakutetezera inu;

6 pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, monga mwa lemba lace, zikhale za pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

7 Ndipo tsiku la khumi la mwezi wacisanu ndi ciwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzicepetse; musamagwira nchito;

8 koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya pfungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi; akhale kwa inu opanda cirema;

9 ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;

10 limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

11 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, pamodzi ndi nsembe yaucimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira.

12 Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi ciwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena, koma mucitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;

13 ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, akhale opanda cirema;

14 ndi nsembe yace yaufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;

15 ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo nao ana a nkhosa khumi ndi anai;

16 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

17 Ndipo tsiku laciwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai a caka cimodzi, opanda cirema;

18 ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

19 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira.

20 Ndi tsiku lacitatu ng'ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai a caka cimodzi opanda cirema;

21 ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

22 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

23 Ndi tsiku lacinai ng'ombe khumi, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

24 nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

25 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

26 Ndi tsiku lacisanu ng'ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

27 ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

28 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

29 Ndi tsiku lacisanu ndi cimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

30 ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

31 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

32 Ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri ng'ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

33 ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

34 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

35 Tsiku lacisanu ndi citatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamacita nchito ya masiku ena;

36 koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri, a caka cimodzi, opanda cirema;

37 nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

38 ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

39 Izi muzikonzera Yehova mu nyengo zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufuru, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.

40 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36