Numeri 20 BL92

Imfa ya Miriamu; madzi a Meriba

1 Ndipo ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, analowa m'cipululu ca Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriamu, naikidwakomweko.

2 Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.

3 Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!

4 Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'cipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?

5 Ndipo munatikwezeranji kutiturutsa m'Aigupto, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.

6 Ndipo Mose ndi Aroni anacoka pamaso pa msonkhano kumka ku khomo la cihema cokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.

7 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

8 Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwaturutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.

9 Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuicotsa pamaso pa Yehova, monga iye anamuuza iye.

10 Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikuturutsireni madzi m'thanthwe umu?

11 Ndipo Mose anasamula dzanja lace, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anaturukamo ocuruka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.

12 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israyeli, cifukwa cace simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali.

13 Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israyeli anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.

Mose apempha njira kwa Aedomu

14 Pamenepo Mose anatumiza amithenga ocokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israyeli, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;

15 kuti makolo athu anatsikira kumka ku Aigupto, ndipo tinakhala m'Aigupto masiku ambiri; ndipo Aaigupto anacitira zoipa ife, ndi makolo athu.

16 Pamenepo tinapfuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natiturutsa m'Aigupto; ndipo, taonani, tiri m'Kadesi, ndiwo mudzi wa malekezero a malire anu.

17 Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wacifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.

18 Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingaturuke kukomana nawe ndi lupanga.

19 Ndipo ana a Israyeli ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wace; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.

20 Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anaturukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.

21 Potero Edomu anakana kulola Israyeli kupitira pa malire ace; cifukwa cace Aisrayeli anampatukira.

Imfa ya Aroni

22 Ndipo anayenda ulendo kucokera ku Kadesi; ndi ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, anadza ku phiri la Hori.

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti,

24 Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israyeli, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.

25 Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wace, nukwere nao m'phiri la Hori;

26 nubvule Aroni zobvala zace, numbveke Eleazara mwana wace; ndipo Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace, nadzafa komweko.

27 Pamenepo Mose anacita monga adamuuza; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse.

28 Ndipo Mose anabvula Aroni zobvala zace, nabveka Eleazara mwana wace; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri, Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.

29 Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36