Numeri 14 BL92

Aisrayeli afuna kubwerera kumka ku Aigupto

1 Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, napfuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.

2 Ndipo ana onse a Israyeli anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m'cipululu muno!

3 Ndipo Yehova atitengeranii kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala cakudya cao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Aigupto?

4 Ndipo anati wina ndi mnzace, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Aigupto.

5 Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israyeli.

6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zobvala zao;

7 nanena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.

8 Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

9 Cokhaci musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawacokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

10 Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala, Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'cihema cokomanako kwa ana onse a Israyeli.

Mose atetezera anthu kwa Mulungu

11 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, cinkana zizindikilo zonse ndinazicita pakati pao?

12 Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwacotsera colowa cao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukuru ndi wamphamvu koposa iwowa.

13 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aaigupto adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwacotsa pakati pao;

14 ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova, ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.

15 Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,

16 Popeza Yehova sanakhoza kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, cifukwa cace anawapha m'cipululu.

17 Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti,

18 Yehova ndiye wolekereza, ndi wa cifundo cocuruka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula woparamula; wakuwalanga ana cifukwa ca mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai.

19 Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa cifundo canu cacikuru, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Aigupto kufikira tsopano.

20 Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako:

21 koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova;

22 popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikilo zanga, ndidazicita m'Aigupto ndi m'cipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;

23 sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;

24 koma mtumiki wanga Kalebi, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zace zidzakhala nalo.

25 Koma Aamaleki ndi Akanani akhala m'cigwamo; tembenukani mawa, nimumke ulendo wanu kucipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

Odandaulawo saloledwa kulowa dziko la Kanani

26 Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,

27 Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israyeli, amene amandidandaulira.

28 Nunene nao, Pali Ine, ati Yehova, ndidzacitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;

29 mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwanu konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;

30 simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

31 Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala cakudya, amenewo ndidzavalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

32 Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno.

33 Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'cipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'cipululu.

34 Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga caka cimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.

35 Ine Yehova ndanena, ndidzacitira ndithu ici khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'cipululu muno, nadzafamo.

36 Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko,

37 amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.

38 Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.

39 Ndipo Mose anauza ana a Israyeli mao onse awa; ndipo anthu anamva cisoni cambiri.

40 Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba pa, phiri, nati, Tiri pano, tidzakwera kumka ku malo amene Yehova ananena; popeza tacimwa.

41 Ndipo Mose anati, Mutero cifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?

42 Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu.

43 Pakuti Aamaleki ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, cifukwa cace Yehova sadzakhala nanu.

44 Koma anakwera pamwamba pa phiri modzikuza; koma likasa la cipangano la Yehova, ndi Mose, sanacoka kucigono.

45 Pamenepo anatsika Aamaleki, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horima.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36