1 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
2 Ndipo Balaki anacita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka pa guwa la nsembe liri lonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo.
3 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo cimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera,
4 Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe liri lonse.
5 Ndipo Yehova anaika mau m'kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene cakuti cakuti.
6 Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yace, iye ndi akalonga onse a Moabu.
7 Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ku Aramu ananditenga Balaki,Mfumu ya Moabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa;Idza, udzanditembererere Yakobo.Idza, nudzanyoze Israyeli.
8 Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberera?Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoza?
9 Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya,Pokhala pa zitunda ndimuyang'ana;Taonani, ndiwo anthu akukhala paokha.Osadziwerengera pakati pa amitundu ena,
10 Adzawerenga ndani pfumbi la Yakobo,Kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israyeli?Ndipo ine ndife monga amafa aongoka mtima,Citsiriziro canga cifanane naco cace!
11 Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandicitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu.
12 Ndipo anayankha nati, Cimene aciika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ici?
13 Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.
14 Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa pa guwa la nsembe liri lonse.
15 Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi iye uko.
16 Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwace, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene cakuti cakuti.
17 Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yace yopsereza, ndi akalonga a Moabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?
18 Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ukani, Balaki, imvani;Ndimvereni, mwana wa Zipori;
19 Mulungu sindiye munthu, kuti aname;Kapena mwana wa munthu, kuti aleke;Kodi anena, osacita?
20 Kapena kulankhula, osacitsimikiza?Taonani, ndalandira mau akudalitsa,Popeza iye wadalitsa, sinditha kusintha.
21 Sayang'anira mphulupulu iri m'Yakobo,Kapena sapenya kupulukira kuli m'lsrayeli.Yehova Mulungu wace ali ndi iye,Ndi mpfuu wa mfumu uli pakati pao,
22 Mulungu awaturutsa m'Aigupto;Mphamvu yace ikunga ya njati.
23 Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo,Kapena ula mwa Israyeli;Pa nyengo yace adzanena kwa Yakobo ndi Israyeli,Cimene Mulungu acita.
24 Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi,Nadzitukumula ngati mkango waumuna:Sugonansokufikira utadya nyama yogwira,Utamwa mwazi wa zophedwa.
25 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse.
26 Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Ciri conse acinena Yehova, comweco ndizicita?
27 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.
28 Ndipo Balaki anamka naye Balamu pamwamba pa Peori, popenyana ndi cipululu.
29 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
30 Ndipo Balaki anacita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe liri laose.