1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonieza cowinda ca Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;
3 azisala vinyo ndi kacasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kacasu wosasa, kapena cakumwa conse ca mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
4 Masiku onse a kusala kwace asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zace kufikira khungu lace,
5 Masiku onse a cowinda cace cakusala, lumo lisapite pamutu pace; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lace zimeretu.
6 Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.
7 Asadzidetse ndi atate wace, kapena mai wace, mbale wace, kapena mlongo wace, akafa iwowa; popeza cowindira Mulungu wace ciri pamutu pace.
8 Masiku onse a kusala kwace akhala wopatulikira kwa Yehova.
9 Munthu akafa cikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wace wowinda; pamenepo azimeta mutu wace tsiku la kumyeretsa kwace, tsiku lacisanu ndi ciwiri aumete.
10 Ndipo tsiku lacisanu ndi citato adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe, ku khomo la cihema cokomanako;
11 ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yaucimo, ndi yina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anacimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wace tsiku lomwelo.
12 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwace, nadze nayo nkhosa yamphongo ya caka cimodzi ikhale nsembe yoparamula; koma masiku adapitawa azikhala cabe, popeza anadetsa kusala kwace.
13 Ndipo cilamulo ca Mnaziri, atatha masiku a kusala kwace ndi ici: azidza naye ku khomo la cihema cokomanako;
14 pamenepo abwere naco copereka cace kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya caka cimodzi yopanda cirema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yamsoti yopanda cirema ikhale nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema ikhale nsembe yoyamika;
15 ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.
16 Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yace yaucimo, ndi nsembe yace yopsereza;
17 naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
18 Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wace wa kusala kwace pa khomo la cihema cokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wace wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.
19 Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa ka m'mtanga, ndi kamtanda kaphanthi kopanda cotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwace;
20 ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ici ncopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.
21 Ici ndi cilamulo ca Mnaziri wakuwinda, ndi ca copereka cace ca Yehova cifukwa ca kusala kwace, pamodzi naco cimene dzanja lace likacipeza; azicita monga mwa cowinda cace anaciwinda, mwa cilamulo ca kusala.
22 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
23 Nena ndi Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Uzidalitsa ana a Israyeli motero; uziti nao,
24 Yehova akudalitse iwe, nakusunge;
25 Yehova awalitse nkhope yace pa iwe, nakucitire cisomo;
26 Yehova akweze nkhope yace pa iwe, nakupatse mtendere.
27 Potero aike dzina langa pa ana a Israyeli; ndipo ndidzawadalitsa.