Numeri 5 BL92

Odetsedwa onse acotsedwe kucigono

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Uza ana a Israyeli kuti aziturutsa m'cigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa cifukwa ca akufa;

3 muwaturutse amuna ndi akazi muwaturutsire kunja kwa cigono, kuti angadetse cigono cao, cimene ndikhala m'kati mwacemo.

4 Ndipo ana a Israyeli anacita cotero, nawaturutsira kunja kwa cigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israyeli anacita.

Za Kubwezera

5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

6 Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwamuna kapena mkazi akacita cimo liri lonse amacita anthu, kucita mosakhulupirika pa Yehova, nakaparamuladi;

7 azibvomereza cimo lace adalicita; nabwezere coparamulaco monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kucipereka kwa iye adamparamulayo.

8 Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere coparamulaco, coparamula acibwezera Yehovaco cikhale ca wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya cotetezerapo, imene amcitire nayo comtetezera.

9 Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zace.

10 Zopatulika za munthu ali yense ndi zace: ziti zonse munthu ali yense akapatsa wansembe, zasanduka zace.

Za mlandu wa nsanje

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

12 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wace, nakamcitira mosakhulupirika,

13 ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wace, ndikumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwira alimkucita;

14 ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti acitire nsanje mkazi wace, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amcitire mkazi wace nsanje angakhale sanadetsedwa;

15 pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wace kwa wansembe, nadze naco copereka cace, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo libano; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yacikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.

16 Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;

17 natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko pfumbi liri pansi m'kacisi, wansembeyo nalithire m'madzimo.

18 Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Mulungu, nabvula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yacikumbutso m'manja mwace, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwace mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.

19 Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagona nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kucidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.

20 Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako;

21 pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'cuuno mwako, ndi kukutupitsa mbulu;

22 ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa mbulu ndi kuondetsa m'cuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.

23 Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

24 Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.

25 Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.

26 Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.

27 Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nacita mosakhulupitika pa mwamuna wace, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa mbulu, ndi m'cuuno mwace mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wace.

28 Koma ngati mkazi sanadetsedwa, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.

29 Ici ndi cilamulo ca nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wace, ampatukira nadetsedwa;

30 kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo acitira mkazi wace nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amcitire cilamulo ici conse.

31 Mwamunayo ndiye wosacita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36