Numeri 26 BL92

Awerenzedwa Aisrayeli

1 Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,

2 Werenga khamu lonse la ana a Israyeli, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli.

3 Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Moabu pa Yordano kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

4 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israyeli, amene adaturuka m'dziko la Aigupto.

5 Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israyeli; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

6 Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.

7 Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu,

8 Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.

9 Ndi ana a Eliyabu: Nemueli, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, mula anatsutsana ndi Yehova;

10 ndipo dziko linayasama pakamwa pace, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja mote unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo cizindikilo.

11 Koma sanafa ana amuna a Kora.

12 Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemueli, ndiye kholo la banja la Anemueli; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

13 Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Sauli, ndiye kholo la banja la Asauli.

14 Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwirikudzamazana awiri.

15 Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Asuni;

16 Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri;

17 Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli.

18 Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.

19 Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.

20 Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.

21 Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.

22 Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.

23 Ana amuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni;

24 Yasubi, ndiye kholo la banja la Ayasubi; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi.

25 Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu.

26 Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yahaliyeli, ndiye kholo la banja la Ayahaliyeli.

27 Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu.

28 Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efraimu.

29 Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Gileadi; ndiye kholo la banja la Agileadi,

30 Ana a Gileadi ndiwo: Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;

31 ndi Asiriyeli, ndiye kholo la banja la Aasiriyeli; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;

32 ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Heferi, ndiye kholo la banja la Aheferi.

33 Ndipo Tselofekadi mwana wa Heferi analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

34 Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

35 Ana amuna a Efraimu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekeri, ndiye kholo la banja la Abekeri; Tahana, ndiye kholo la banja la Atahana.

36 Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani.

37 Iwo ndiwo mabanja a ana a Efraimu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.

38 Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibeli, ndiye kholo la banja la Aasibeli; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu;

39 Sufamu ndiye kholo la banja la Asufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu.

40 Ndipo ana amuna a Bela ndiwo Aridi ndi Namani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Namani, ndiye kholo la banja la Anamani.

41 Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.

42 Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ace ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.

43 Mabanja aose a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai.

44 Ana amuna a Aseri monga mwa mabanja ao ndiwo: Yimna, ndiye kholo la banja la Ayimna; Yisivi, ndiye kholo la banja la Ayisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya.

45 Ana a Beriya ndiwo: Heberi, ndiye kholo la banja la Aheberi; Malikiyeli, ndiye kholo la banja la Amalikiyeli.

46 Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Aseri ndiye Sera.

47 Iwo ndiwo mabanja a ana amuna a Aseri monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

48 Ana amuna a Nafitali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeli, ndiye kholo la banja la Ayazeli; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni;

49 Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu.

50 Iwo ndiwo mabanja a Nafitali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.

51 Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israyeli, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

Magawidwe a dziko

52 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

53 Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale colowa cao.

54 Ocurukawo, uwacurukitsire colowa cao; ocepawo uwacepetsere colowa cao; ampatse yense colowa cace monga mwa owerengedwa ace.

55 Koma aligawe ndi kucita maere; colowa cao cikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao,

56 Agawire ocuruka ndi ocepa colowa cao monga mwa kucita maere.

57 Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Gerisoni, ndiye kholo la banja la Agerisoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.

58 Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akohati. Ndipo Kohati anabala Amiramu.

59 Ndipo dzina lace la mkazi wace wa Amiramu ndiye Yokebedi, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Aigupto; ndipo iye anambalira Amiramu Aroni ndi Mose, ndi Miriamu mlongo wao.

60 Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara anabadwira Aroni.

61 Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wacilendo pamaso pa Yehova.

62 Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwa pakati pa ana a Israyeli; cifukwa sanawapatsa colowa mwa ana a Israyeli.

63 Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israyeli m'zidikha za Moabu ku Yordano pafupi pa Yeriko.

64 Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israyeli m'cipululu ca Sinai.

65 Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'cipululu. Ndipo sanatsalira mmodzi wa iwowa koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36