Numeri 17 BL92

Ndodo ya Aroni iphuka

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi ana a Israyeli, nulandire kwa yense ndodo, banja liri onse la makolo ndodo imodzi, mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yace.

3 Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkuru yense wa nyumba za makolo ao.

4 Ndipo uziike m'cihema cokomanako, cakuno ca mboni, kumene ndikomana ndi inu.

5 Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israyeli amene adandaula nao pa inu.

6 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.

7 Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'cihema ca mboni.

8 Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose analowa m'cihema ca mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nicita maluwa, nipatsa akatungurume.

9 Ndipo Mose anaturutsa ndodo zonse kuzicotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israyeli; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yace.

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kulika cakuno ca mboni, isungike ikhale cizindikilo ca pa ana opikisana; kuti unelitsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.

11 Ndipo Mose anacita monga Yehova adamuuza, momwemo anacita.

12 Pamenepo ana a Israyeli ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.

13 Yense wakuyandikiza kacisi wa Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36