Numeri 1 BL92

Aisrayeli awerengedwa m'cipululu ca Sinai

1 NDIPO Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, m'cihema cokomanako, tsiku loyamba la mwezi waciwiri, caka caciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto, ndi kuti,

2 Werenga khamu lonse la ana a Israyeli, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzi mmodzi.

3 Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israyeli akuturuka kunkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu,

4 Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mapfuko onse; yense mkuru wa nyumba ya kholo lace.

5 Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.

6 Wa Simeoni, Selumiyeli mwana wa Zurisadai.

7 Wa Yuda, Nahesoni mwana wa Aminadabu.

8 Wa Isakara, Netaneli mwana wa Zuwara.

9 Wa Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.

10 Wa ana a Yosefe: wa Efraimu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

11 Wa Benjamini, Abidana mwana wa Gideoni.

12 Wa Dani, Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

13 Wa Aseri, Pagiyeli mwana wa Okirani.

14 Wa Gadi, Eliyasafe mwana wa Deyueli.

15 Wa Nafitali, Ahira mwana wa Enani.

16 Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mapfuko a makolo ao; ndiwo akuru a zikwizo za Israyeli.

17 Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao;

18 nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi waciwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kuchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzi mmodzi.

19 Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'cipululu ca Sinai.

20 Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israyeli, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

21 owerengedwa ao a pfuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.

22 A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

23 owerengedwa ao a pfuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

24 A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

25 owerengedwa ao a pfuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

26 A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makomi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

27 owerengedwa ao a pfuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

28 A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

29 owerengedwa ao a pfuko la lsakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.

30 A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

31 owerengedwa ao a pfuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

32 A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efraimu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

33 owerengedwa ao a pfuko la Efraimu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.

34 A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

35 owerengedwa ao a pfuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.

36 A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

37 owerengedwa ao a pfuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.

38 A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

39 owerengedwa ao a pfuko la Dani, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

40 A ana a Aseri, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

41 owerengedwa ao a pfuko la Aseri, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu.

42 A ana a Nafitali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;

43 owerengedwa ao a pfuko la Nafitali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

44 Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israyeli, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lace.

45 Potero owerengedwa onse a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli;

46 inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

Alevi sawerengedwa

47 Koma Alevi monga mwa pfuko la makolo ao sanawerengedwa mwa iwo.

48 Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti,

49 Pfuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israyeli;

50 koma iwe, uike Alevi asunge kacisi wa mboni, ndi zipangizo zace zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula kacisi, ndi zipangizo zace zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa kacisi.

51 Ndipo akati amuke naye kacisiyo, Aleviamgwetse, ndipo akati ammange, Alevi amuimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe,

52 Ndipo ana a Israyeli amange mahema ao, yense ku cigono cace, ndi yense ku mbendera yace, monga mwa makamu ao.

53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa kacisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israyeli; ndipo Alevi azidikira kacisi wa mboni.

54 Momwemo ana a Israyeli anacita monga mwa zonse Yehova adauza Mosel anacita momwemo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36