1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Uza ana a Israyeli, nuti nao, Muzisamalira kubwera naco kwa Ine copereka canga, cakudya canga ca nsembe zanga zamoto, ca pfungo lokoma, pa nyengo yace yoikika.
3 Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: ana a nkhosa awiri a caka cimodzi opanda cirema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.
4 Mwana wa nkhosa mmodziyo umpereke m'mawa, ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo;
5 ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la bini wa mafuta opera.
6 Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika ku phiri la Sinai, icite pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
7 Ndi nsembe yace yothira ya mwana wa nkhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la bini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya cakumwa colimba.
8 Ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yace, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.
9 Ndipo dzuwa la Sabata ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, opanda cirema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yace yothira;
10 ndiyo nsembe yopsereza ya dzuwa la Sabata liri lonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.
11 Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi opanda cirema;
12 ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iri yonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;
13 ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwana wa nkhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya pfungo lokoma, nsembe yamoto ya. Yehova.
14 Ndipo nsembe zace zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la bini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwana wa nkhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uli wonse kunena miyezi yonse ya caka.
15 Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yaucimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.
16 Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, pali paskha wa Yehova.
17 Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi uwu pali madyerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda cotupitsa.
18 Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena;
19 koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi; akhale kwa inu opanda cirema;
20 ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;
21 upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi; uzitero ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;
22 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, yakutetezera inu.
23 Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza ya m'mawa, ndiyo ya nsembe yopsereza kosalekeza.
24 Momwemo mupereke cakudya ca nsembe yamoto ca pfungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, cakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.
25 Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.
26 Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'madyerero anu a masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.
27 Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya pfungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi;
28 ndi nsembe yace ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi,
29 limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;
30 tonde mmodzi wakutetezera inu.
31 Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, zikhale kwa inu zopanda cirema, ndi nsembe zace zothira.