1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Uza ana Israyeli, nunene nao, Mutalowa a m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale colowa canu, dziko ija Kanani monga mwa malire ace,
3 dera lanu la kumwela lidzakhala locokera ku cipululu ca Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwela adzakhala ocokera ku malekezero a Nyanja ya Mcere kum'mawa;
4 ndi malire anu adzapinda kucokera kumwela kumka pokwera Akrabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kuturuka kwace adzacokera kumwela ku Kadesi Barinea, nadzaturuka kumka ku Hazara Adara, ndi kupita kumka ku Azimoni;
5 ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kumka ku mtsinje wa Aigupto, ndi kuturuka kwao adzaturuka kunyanja.
6 Kunena za malire a kumadzulo, nyanja yaikuru ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.
7 Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku nyanja yaikuru mulinge ku phiri la Hori:
8 kucokera ku phiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kuturuka kwace kwa malire kudzakhala ku Zedadi.
9 Ndipo malirewo adzaturuka kumka ku Zifironi, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Hazara Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
10 Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ocokera ku Hazara Enani kumka ku Sefamu;
11 ndi malire adzatsika ku Sefamu kumka ku Ribala, kum'mawa kwa Ayina; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
12 ndi malire adzatsika ku Yordano, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Nyanja ya Mcere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ace polizinga.
13 Ndipo Mose anauza ana a Israyeli, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kucita maere, limene Yehova analamulira awapatse mapfuko asanu ndi anai ndi hafu;
14 popeza pfuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi pfuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi pfuko la hafu la Manase lalandira colowa cao;
15 mapfuko awiriwa ndi hafu adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano ku Yeriko, kum'mawa, koturukira dzuwa.
16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
17 Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale colowa canu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18 Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku pfuko limodzi, agawe dziko likhale colowa cao.
19 Maina a amunawo ndiwo: wa pfuko la Yuda, Kalebi mwana wa Yefune.
20 Wa pfuko la ana a Simeoni, Semuyeli mwana wa Amihudi.
21 Wa pfuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.
22 Wa pfuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili.
23 Wa ana a Yosefe; wa pfuko la ana a Manase, kalonga Haniyeli mwana wa Efodi.
24 Wa pfuko la ana a Efraimu, kalonga Kemuyeli mwana wa Sipitana.
25 Wa pfuko la ana a Zebuloni, kalonga Elisafana mwana wa Paranaki.
26 Wa pfuko la ana a Isakara, kalonga Palitiyeli mwana wa Azana.
27 Wa pfuko la ana a Aseri, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi.
28 Wa pfuko la ana a Nafitali, kalonga Pedaheli mwana wa Amihudi.
29 Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israyeli colowa cao m'dziko la Kanani.