1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ace; ucite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.
3 Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la cihema cokomanako,
4 Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akuru a zikwi a m'Israyeli, azisonkhana kuli iwe.
5 Mukaliza cokweza, ayende a m'zigono za kum'mawa.
6 Mukalizanso cokweza, a m'zigono za kumwela ayende; alize cokweza pakumuka.
7 Pomemeza msonkhano mulize, wosati cokweza ai.
8 Ana amuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.
9 Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kucita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize cokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukila inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.
10 Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu cikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11 Ndipo kunacitika, caka caciwiri, mwezi waciwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kucokera kwa kacisi wa mboni.
12 Ndipo ana a Israyeli anayenda monga mwa maulendo ao, kucokera m'cipululu ca Sinai; ndi mtambo unakhala m'cipululu ca Parana.
13 Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
14 Ndipo anayamba kuyenda a mbendera ya cigono ca ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lace ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu.
15 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Isakara panali Netaneli mwana wa Zuwara.
16 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.
17 Ndipo anagwetsa kacisi; ndi ana a Gerisoni, ndi ana a Merari, akunyamula kacisi, anamuka naye.
18 Ndi a mbendera ya cigono ca Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lace anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri.
19 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Simeoni anayang'anira Selumiyeli mwana wa Zurisadai.
20 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafe mwana wa Deyueli.
21 Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu kacisi asanafike iwowa.
22 Ndipo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Efraimu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Elizama mwana wa Amihudi.
23 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Manase anayang'anira Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.
24 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Benjamini anayang'anira Abidana mwana wa Gideoni.
25 Pamenepo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
26 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Aseri anayang'anira Pagiyeli mwana wa Okirani.
27 Ndi pa gulu la pfuko la ana a Nafitali anayang'anira Ahira mwana wa Enani.
28 Potero maulendo a ana a Israyeli anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendowao.
29 Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reueli Mmidyani mpongozi wa Mose, Ife tirikuyenda kumka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakucitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israyeli zokoma.
30 Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.
31 Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'cipululu, ndipo udzakhala maso athu.
32 Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma ziri zonse Yehova aticitira ife, zomwezo tidzakucitira iwe.
33 Ndipo anayenda kucokera ku phiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la cipangano ca Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
34 Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kucokera kucigono.
35 Ndipo kunali pakucoka kumka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.
36 Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwi zikwi za Israyeli.