Numeri 31 BL92

Aisrayeli agonjetsa Amidyani

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Abwezereni cilango Amidyani cifukwa ca ana a Israyeli; utatero udzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wako.

3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidyani, kuwabwezera Amidyani cilango ca Yehova.

4 Muwatume kunkhondo a pfuko limodzi, cikwi cimodzi, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, atere mafuko onse a Israyeli.

5 Ndipo anapereka mwa zikwi za Israyeli, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.

6 Ndipo Mose anawatuma a pfuko limodzi cikwi cimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Pinehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lace.

7 Ndipo anawathira nkhondo Amidyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.

8 Ndipo anapha mafumu a Amidyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekamu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.

9 Ndipo ana a Israyeli anagwira akazi a Amidyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi cuma cao conse.

10 Ndipo anatentha ndi moto midzi yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.

11 Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.

12 Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israyeli, kucigono, ku zidikha za Moabu, ziri ku Yordano pafupi pa Yeriko.

Mayeretsedwe a ankhondowo

13 Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anaturuka kukomana nao kunja kwa cigono.

14 Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.

15 Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse?

16 Taonani, awa analakwitsa ana a Israyeli pa Yehova nilica Peoricija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.

17 Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye.

18 Koma ana akazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeru ndi moyo akhale anu.

19 Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ali yense adapha munthu, ndi ali yense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lacitatu ndi lacisanu ndi ciwiri, inu ndi andende anu.

20 Muyeretse zobvala zanu zonse, zipangizo zonse zacikopa, ndi zaomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse zamtengo.

21 Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la cilamuloco Yehova analamulira Mose ndi ili:

22 Golidi, ndi siliva, mkuwa, citsulo, ndolo ndi mtobvu zokha,

23 zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.

24 Ndipo muzitsuke zobvala zanu tsiku lacisanu ndi ciwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m'cigono.

Magawidwe a zofunkha

25 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

26 Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe; ndi Eleazara wansembe, ndi akuru a nyumba za makolo za khamulo;

27 nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anaturuka kunkhondo, ndi khamu lonse.

28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akuturuka kunkhondo apereke kwa Yehova; munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.

29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.

30 Ndipo ku gawo la ana a Israyeli utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova.

31 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anacita monga Yehova anamuuza Mose.

32 Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,

33 ndi ng'ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri,

34 ndi aburu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu cimodzi,

35 ndi anthu, ndiwo akazi osadziwa mwamuna mogona naye, onse pamodzi zikwi makumi atatu ndi ziwiri.

36 Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adaturuka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.

37 Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.

38 Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.

39 Ndipo aburu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.

40 Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.

41 Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

42 Ndipo kunena za gawo la ana a Israyeli, limene Mose adalicotsa kwa anthu ocita nkhondowo,

43 (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,

44 ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi,

45 ndi aburu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,

46 ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi,)

47 mwa gawolo la ana a Israyeli Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Zopereka zaufulu za akazembe

48 Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;

49 nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowa munthu mmodzi wa ife.

50 Ndipo tabwera naco copereka ca Yehova, yense cimene anacipeza, zokometsera zagolidi, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kucita cotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.

51 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golidiyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.

52 Ndipo golidi yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.

53 Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.

54 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golidi kwa akuru a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku cihema cokomanako, cikumbutso ca ana a Israyeli pamaso pa Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36