1 Koma ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazeri, ndi dziko la Gileadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.
2 Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,
3 Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazeri, ndi Nimra, ndi Heseboni, ndi Eleyali, ndi Sebamu, ndi Nebo, ndi Beoni,
4 dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israyeli, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.
5 Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale lao lao; tisaoloke Yordano.
6 Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?
7 Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israyeli kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?
8 Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza acoke ku Kadesi Barinea kukaona dziko.
9 Popeza atakwera kumka ku cigwa ca Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israyeli, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.
10 Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira iye, nati,
11 Anthu adakwerawo kuturuka m'Aigupto, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo; popeza sananditsata Ine ndi mtima wonse;
12 koma Kalebi mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.
13 Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israyeli, nawayendetsa-yendetsa m'cipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udacita coipa pamaso pa Yehova.
14 Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ocimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israyeli,
15 Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata iye, adzawasiyanso m'cipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.
16 Ndipo anayandikiza, nati, Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israyeli, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao;
17 ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga cifukwa ca okhala m'dzikomo.
18 Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israyeli atalandira yense colowa cace.
19 Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordano, ndi m'tsogolo mwace; popeza colowa cathu tacilandira tsidya lino la Yordano kum'mawa.
20 Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzacita ici, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,
21 ndi kuoloka Yordano pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapitikitsa adani ace pamaso pace,
22 ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osacimwira Yehova ndi Israyeli; ndipo dziko ili lidzakhala lanu lanu pamaso pa Yehova.
23 Koma mukapanda kutero, taonani, mwacimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti cimo lanu lidzakupezani.
24 Dzimangireni midzi ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzicite zoturuka m'kamwa mwanu.
25 Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzacita monga mbuyanga alamulira.
26 Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'midzi ya ku Gileadi;
27 koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.
28 Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akuru a makolo a mapfuko a ana a Israyeli za iwo.
29 Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordano, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Gileadi likhale lao lao;
30 koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko ao ao pakati pa inu m'dziko la Kanani.
31 Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzacita.
32 Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma colowa cathu cathu cikhale tsidya lino la Yordano.
33 Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi pfuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, dzikoli ndi midzi yace m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako,
34 Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroeri;
35 Ataroti Sofani, Yazeri, ndi Yogebeha;
36 ndi Beti Nimira, ndi Beti Harani: midzi ya m'malinga, ndi makola a zoweta.
37 Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyali, ndi Kiriyataimu;
38 ndi Nebo, ndi Baala Meoni (nasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaicha midzi adaimanga ndi maina ena.
39 Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase anamka ku Gileadi, naulanda, napitikitsa Aamori anali m'mwemo.
40 Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Gileadi; ndipo anakhala m'menemo.
41 Ndipo Yairi mwana wa Manase anamka nalanda midzi yao, naicha Havoti Yairi. Ndipo Noba anamka nalanda Kenati, ndi miraga yace, naucha Noba, dzina lace.