Numeri 22 BL92

Za Balamu ndi Balaki

1 Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Moabu, tsidya la Yordano ku Yeriko.

2 Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israyeli anacitira Aamori.

3 Ndipo Moabu anacita mantha akuru ndi anthuwo, popeza anacuruka; nada mtima Moabu cifukwa ca ana a Israyeli.

4 Ndipo Moabu anati kwa akuru a Midyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse ziri pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Moabu masiku amenewo.

5 Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wace, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anaturuka anthu m'dziko la Aigupto; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

6 Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawalaka, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapitikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

7 Ndipo akuru a Moabu ndi akuru a Midyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

8 Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Moabu anagona ndi Balamu.

9 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?

10 Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Moabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,

11 Taonani, anthu awa adaturuka m'Aigupto aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapitikitsa.

12 Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.

13 Ndipo Balamu anauka m'mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu,

14 Pamenepo akalonga a Moabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati, Alikukana Balamu kudza nafe.

15 Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ocuruka, ndi omveka koposa awa.

16 Ndipo anadza kwa Balamu, nati kwa iye, Atero Balaki mwana wa Zipori, Pasakhaletu cinthu cakukuletsa kudza kwa ine;

17 popeza ndidzakucitira ulemu waukuru, ndipo zonse unena ndi ine ndidzacita; cifukwa cace idzatu, unditembererere anthu awa.

18 Ndipo Balamu, anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Cinkana Balaki andipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kucepsako kapena kuonjezako.

19 Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe comwe Yehova adzanenanso nane.

20 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kumka nao, koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukacite.

21 Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga buru wace, namuka nao akalonga a ku Moabu.

22 Koma anapsa mtima Mulungu cifukwa ca kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye, Ndipo anali wokwera pa buru wace, ndi anyamata ace awiri anali naye,

23 Ndipo buruyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lace ku dzanja lace; ndi buru anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda buru kumbwezera kunjira.

24 Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali yina kuli linga, mbali yina linga.

25 Ndipo buru anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.

26 Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.

27 Ndipo buru wace anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pace; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda buru ndi ndodo.

28 Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pace pa buru, nati uyu kwa Balamu, Ndakucitanji, kuti wandipanda katatu tsopano?

29 Pamenepo Balamu anati kwa buru, Cifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.

30 Ndipo buru anati kwa Balamu, Si ndine buru wako amene umayenda wokwera pa ine ciyambire ndiri wako kufikira lero lino? Kodi ndikakucitira cotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.

31 Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola liri kudzanja, ndipo anawerama mutu wace, nagwa nkhope yace pansi.

32 Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji buru wako katatu tsopano? taona, ndaturuka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa camtu pamaso panga;

33 koma buru anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.

34 Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndacimwa, popeza sindinadziwa kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati cikuipirani, ndibwerera.

35 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene, Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.

36 Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamturukira kukakomana naye ku mudzi wa Moabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ace.

37 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumiza kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? sindikhoza kodi kukucitira ulemu?

38 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndiri nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.

39 Ndipo Balamu anamuka ndi Balaki, nafika iwo ku Kiriyati Huzoti.

40 Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye.

41 Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera nave ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36