Numeri 30 BL92

Za cowinda cocita akazi

1 Ndipo Mose ananena ndi akuru a mapfuko a ana a Israyeli, nati, Cinthu anacilamulira Yehova ndi ici:

2 Munthu akacitira Yehovacowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wace codziletsa, asaipse mau ace; azicita monga mwa zonse zoturuka m'kamwa mwace.

3 Ndipo mkazi akacitira Yehova cowinda, nakadzimanga naco codziletsa, pokhala ali m'nyumba ya atate wace, m'unamwali;

4 ndipo atate wace akamva cowinda cace, ndi codziletsa cace anamanga moyo wace naco, koma wakhala naye cete atate wace; pamenepo zowinda zace zonse zidzakhazikika, ndi codziletsa ciri: conse wamanga naco moyo wace cidzakhazikika.

5 Koma atate wace akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zace zonse, ndi zodziletsa zace zonse anamanga nazo moyo wace, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wace anamletsa.

6 Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zace, kapena zonena zopanda pace za milomo yace, zimene anamanga nazo moyo wace;

7 nakazimva mwamuna wace, nakakhala naye cete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zace zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.

8 Kama mwamuna wace akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza cowinda cace anali naco, ndi zonena zopanda pace za milomo yace, zimene anamanga nazo moyo wace; ndipo Yehova adzamkhululukira.

9 Koma cowinda ca mkazi wamasiye, kapena mkazi wocotsedwa, ziti zonse anamanga nazo moyo wace zidzamkhazikikira.

10 Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wace, kapena anamanga moyo wace ndi codziletsa ndi kulumbirapo,

11 ndipo mwanuna wace anamva, koma anakhala naye cete osamletsa, pamenepo zowinda zace zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.

12 Koma ngati mwamuna wace anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zoturuka m'milomo yace kunena za zowinda zace, kapena za codziletsa ca moyo wace sizidzakhazikika; mwamuna wace anazifafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira Iye.

13 Cowinda ciri conse, ndi columbira ciri conse codziletsa cakucepetsa naco moyo, mwamuna wace acikhazikira, kapena mwamuna wace acifafaniza.

14 Koma mwamuna wace akakhala naye cete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zace zonse, kapena zodziletsa zace zonse, ziri pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye cete tsikuli anazimva iye.

15 Koma akazifafaniza atatha kuzimva; pamenepo adzasenza mphulupulu yace.

16 Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wace, pakati pa atate ndi mwana wace wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36