Levitiko 27 BL92

Cowinda ndi ciombolo cace

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Pamene munthu acita cowinda ca padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako.

3 Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu a siliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

4 Koma akakhala wamkazi, umuyesere wa masekeli makumi atatu.

5 Akakhala munthu wa zaka zisanu kufikira wina wa zaka makumi awiri uwayesere, wamwamuna wa masekeli makumi awiri, ndi wamkazi wa masekeli khumi.

6 Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva.

7 Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi.

8 Koma cuma cace cikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.

9 Ndipo cikakhala ca nyama imene anthu amabwera nayo ikhale copereka ca Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.

10 Asaisinthe, yokoma m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m'malo mwa inzace, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika.

11 Ndipo cikakhala ca nyama yodetsa, imene sabwera nayo ikhale copereka ca Yehova, aike nyamayi pamaso pa wansembe;

12 ndipo wansembeyo aiyese mtengo wace, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga uiyesa wansembewe, momwemo.

13 Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wace.

14 Munthu akapatula nyumba yace ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wace, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.

15 Ndipo iye wakuipatula akaombola nyumba yace, aonjezepo limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo idzakhala yace.

16 Munthu akapatulirako Yehova munda wace wace, uziuyesa monga mwa mbeu zace zikakhala; homeri wa barie uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.

17 Akapatula munda wace kuyambira caka coliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.

18 Akaupatula munda wace citapita caka coliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira caka coliza lipenga, nazicepsako pa kuyesa kwako.

19 Ndipo wakupacula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wace.

20 Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;

21 koma poturuka m'caka coliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; ukhale wace wace wa wansembe.

22 Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wace wace;

23 pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wace wa kuyesa kwako kufikira caka coliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, cikhale cinthu copatulikira Yehova,

24 Caka coliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lace lace.

25 Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika; sekeli ndi magera makumi awiri.

26 Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

27 Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wace; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.

Za coperekedwa ciperekere, ndi Lakhumi La za nthaka ndi za m'khola

28 Koma asacigulitse kapena kuciombola cinthu coperekedwa ciperekere kwa Mulungu, cimene munthu acipereka ciperekere kwa: Yehova, cotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wace wace; ciri conse coperekedwa ciperekere kwa Mulungu neopatulikitsa.

29 Asamuombole munthu woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.

30 Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zace za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.

31 Koma munthu akaombolatu kanthu ka limodzi la magawo khumiwo aonjezeko limodzi la magawo asanu.

32 Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, ziri zonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhale lopatulikira Yehova.

33 Asafunse ngati yabwino kapena yoipa, kapena kuisintha; koma akaisinthatu, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika zonse ziwiri; asamaiombola.

34 Awa ndi malamulo, amene Yehova anauza Mose, awauze ana a Israyeli, m'phiri la Sinai.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27