1 Mose ndi Aroni, nati,
2 Nenani nao ana a Israyeli, nimuti nao, Pamene mwamuna ali yense ali ndi nthenda yakukha m'thupi mwace, akhale wodetsedwa, cifukwaca kukha kwace.
3 Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwace ndiko: ngakhale cakukhaco cituruka m'thupi mwace, ngakhale caleka m'thupi mwace, ndiko kumdetsa kwace.
4 Kama ali yense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi cinthu ciri conse acikhalira ciri codetsedwa.
5 Ndipo munthu ali yense wakukhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo,
6 Ndipo iye wakukhalira cinthu ciri conse adacikhalira wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
7 Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
8 Ndipo wakukhayo akalabvulira wina woyera; pamenepo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
9 Ndipo mbereko iri yonse akwerapo wakukhayo iri yodetsedwa.
10 Ndipo munthu ali yense akakhudza kanthu kali konse kadali pansi pace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
11 Ndipo munthu ali yense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
12 Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi.
13 Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwace, natsuke zobvala zace; nasambe thupi lace ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.
14 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la cihema cokomanako, nazipereke kwa wansembe;
15 ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yaucimo, ndi yina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova cifukwa ca kukha kwace.
16 Ndipo munthu ali yense akagona uipa, azisamba thupi lace lonse ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
17 Ndipo cobvala ciri conse, ndi cikopa ciri conse, anagona uipa pamenepo azitsuke ndi madzi, nizidzakhala zodetsedwa kufikira madzulo.
18 Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
19 Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwace nkwa mwazi m'thupi mwace, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo ali yense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
20 Ndipo cinthu ciri conse agonapo pokhala ali padera ncodetsedwa; ndi cinthu ciri conse akhalapo ncodetsa.
21 Ndipo ali yense akhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
22 Ndipo ali yense akhudza cinthu ciri conse akhalapo iye, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
23 Ndipo cikakhala pakama, kapena pa cinthu ciri conse akhalapo iye, atacikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
24 Ndipo ngati mwamuna ali yense agona naye, ndi kudetsa kwace kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama ali yense agonapo ali wodetsedwa.
25 Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwace, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwace; masiku onse cirinkukha comdetsa cace, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwace.
26 Kama ali yense agonapo masiku a kukha kwace akhale ngati kama wa kuoloka kwace; ndi cinthu ciri conse akhalapo ciri codetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwace.
27 Ndipo munthu ali yense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28 Koma akayeretsedwa kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri, ndipo atatero adzakhala woyeretsedwa.
29 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la cihema cokomanako.
30 Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yaucimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova cifukwa ca kukha kwace komdetsa.
31 Motero muzipatula ana a Israyeli kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa kacisi wanga ali pakati pao.
32 Ici ndi cilamulo ca wakukha, ndi ca iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa;
33 ndi ca mkazi alinkudwala ndi kudetsedwa kwace, ndi ca iye alikukha kapena mwamuna, kapena mkazi, ndi ca iye agona ndi mkazi wodetsedwa.