Levitiko 17 BL92

Popereka nsembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana a Israyeli onse, nuti nao, Ici ndi cimene Yehova wauza, ndi kuti,

3 Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli akapha ng'ombe, kapena mwana wa nkhosa, kapena mbuzi, m'cigono, kapena akaipha kunja kwa cigono,

4 osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti aipereke copereka ca Yehova, ku bwalo la kacisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wocimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace;

5 kotero kuti ana a Israyeli azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.

6 Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la cihema cokomanako, natenthe mafuta akhale pfungo lokoma lokwera kwa Yehova.

7 Ndipo asamapheranso ziwanda nsembe zao, zimene azitsata ndi cigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.

8 Ndipo uzinena nao, Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,

9 osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

Aletsedwa kudya mwazi

10 Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

11 Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, ucite cotetezera moyo wanu; pakuti wocita cotetezera ndiwo mwazi, cifukwa ca moyo wace.

12 Cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo ali yense wakugoneramwa inu asamadya mwazi.

13 Ndipo munthu ali yense wa ana a Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wace naufotsere ndi dothi.

14 Pakuti ndiwo moyo wa: nyama zonse, mwazi wace ndiwo moyo wace; cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Musamadya mwazi wa nyama iri yonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wace; ali yense akaudya adzasadzidwa.

15 Ndipo ali yense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsaru zace, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.

16 Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lace, adzasenza mpholupulu yace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27