Levitiko 8 BL92

Kupatulidwa kwa ansembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Tenga Aroni ndi ana ace pamodzi naye ndi zobvalazo, ndi mafuta odzozawo, ndi ng'ombe ya nsembe yaucimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsawo;

3 nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la cihema cokomanako.

4 Ndipo Mose anacita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la cihema cokomanako.

5 Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ici ndi cimene Yehova adauza kuti cicitike.

6 Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ace, nawasambitsa ndi madzi,

7 Ndipo anambveka ndi maraya a m'kati, nammanga m'cuuno ndi mpango, nambveka ndi mwinjiro, nambveka ndi efodi, nammanga m'cuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pace.

8 Ndipo anamuika capacifuwa; naika m'capacifuwa Urimu ndi Tumimu.

9 Naika nduwirayo pamutu pace; ndi panduwira, pamphumi pace anaika golidi waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

10 Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza kacisi, ndi ronse ziti m'mwemo, nazipatula.

11 Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace, kuzipatula.

12 Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula,

13 Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawabveka maraya a m'kati, nawamanga m'cuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adauza Mose.

14 Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yaucimo.

15 Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi cala cace pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alicitire colitetezera.

16 Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe.

17 Koma ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi nyama yace, ndi cipwidza cace, anazitentha ndi mote kunja kwa cigono; monga Yehova adamuuza Mose.

18 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.

19 Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

20 Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zace; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.

21 Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Kupatulidwa kwa Aroni ndi ana ace

22 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.

23 Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wace naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa cala cacikuru ca ku dzanja lamanja lace, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja.

24 Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa cala cacikuru ca ku dzanja lamanja lao, ndi pacala cacikuru ca phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira,

25 Ndipo anatenga mafutawo ndi mcira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

26 ndipo mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

27 anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ace amuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

28 Pamenepo Mose anazicotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

29 Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zobvala zace, ndi pa ana ace amuna, ndi pa zobvala za ana ace amuna omwe; napatula Aroni, ndi zobvala zace, ndi ana ace amuna, ndi zobvala za ana ace amuna omwe.

31 Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa cihema cokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu mtanga wa nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ace aidye.

32 Koma cotsalira ca nyama ndi mkate mucitenthe ndi moto.

33 Ndipo musaturuka pa khomo la cihema cokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.

34 Monga anacita lero lino, momwemo Yehova anauza kucita, kukucitirani cotetezera.

35 Ndipo mukhale pakhomo pa cihema cokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga cilangizo ca Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.

36 Ndipo Aroni ndi ana ace amuna anacita zonse zimene Yehova anauza pa dzanja la Mose.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27