Levitiko 13 BL92

Malamulo a pa nthenda yakhate

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ngati munthu ali naco cotupa, kapena nkhanambo, kapena cikanga pa khungu la thupi lace, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lace, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ace ansembe;

3 ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lace, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namuche wodetsedwa.

4 Koma ngati cikanga cikhala cotuwa pa khungu la thupi lace, ndipo cikaoneka cosapitirira khungu, ndi tsitsi lace losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;

5 ndipo wansembe amuonenso tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;

6 ndipo wansembe amuonenso tsikulacisanu ndi ciwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amuche iye woyera, ndiyo nkhanambo cabe; ndipo atsuke zobvala zace, ndiye woyera;

7 koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsakwa wansembe kuti achedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;

8 ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amuche wodetsedwa, ndilo khate.

9 Pamene nthenda yakhate iri mwa munthu, azimfikitsa kwa wansembe;

10 ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali cotupa coyera pakhungu, ndipo casanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pacotupa pali mnofu wofiira,

11 ndilo khate lakale pa khungu la thupi lace, ndipo wansembe amuche wodetsedwa; asambindikiritse popeza ali wodetsedwa.

12 Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wace kufikira mapazi ace, monga momwe apenyera wansembe;

13 pamenepo wansembe aone, ndipo taonani, ngati khate lakuta thupi lace, amuche woyera wanthendayo; patuwa ponsepo; ndiye woyera.

14 Koma tsiku liri lonse ukaoneka pa iye mnofu wofiira, adzakhala wodetsedwa,

15 Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namuche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate.

16 Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,

17 ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amuche woyera wanthendayo; ndiye woyera.

18 Ndipo pamene thupi liri ndi cironda pakhungu pace, ndipo capola,

19 ndipo padali cironda pali cotupa coyera, kapena cikanga cotuuluka, pamenepo acionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone,

20 ndipo taonani, ngati cioneka cakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lace lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'cirondamo.

21 Koma wansembe akaciona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sicinakumba kubzola khungu, koma cazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

22 ndipo ngati capitirira khungu, wansembe amuche wodetsedwa; ndilo khate.

23 Koma ngati cikanga caima pomwepo, cosakula, ndico cipsera ca cironda; ndipo wansembe amuche woyera.

24 Kapena pamene thupi lidapsya ndi mota pakhungu pace, ndipo mnofu wofiira wakupsyawo usanduka cikanga cotuuluka, kapena cotuwa:

25 pamenepo wansembe acione; ndipo taonani, ngati tsitsi la cikanga lasanduka lotuwa, ndipo cioneka cakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsyamo; ndipo wansembe azimucha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.

26 Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m'cikangamo, ndipo sicikumba kubzola khungu, koma cazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

27 ndipo wansembe amuone tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati cakula pakhungu, wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate,

28 Ndipo ngati cikanga ciima pomwepo, cosakula pakhungu koma cazimba; ndico cotupa ca kupsya; ndipo wansembe amuche woyera; pakuti ndico cipsera ca kupsya.

29 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandebvu,

30 wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndebvu.

31 Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri;

32 ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,

33 pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena;

34 ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amuche woyera, ndipo iye atsuke zobvala zace, nakhala woyera.

35 Koma ngati mfundu ikula pakhungu atachedwa woyera;

36 pamenepo wansembe amuone, ndipo taonani, ngati mfundu yakula pakhungu, wansembe asafunefune tsitsi loyezuka, ndiye wodetsedwa.

37 Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amuche woyera.

38 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi zikanga pa khungu la thupi lace, zikanga zoyerayera;

39 wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga ziri pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera.

40 Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera.

41 Ndipo ngati tsitsi lathothoka pamphumi pace ndiye wa masweswe, koma woyera.

42 Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lace la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lirikubuka pakati pa dazi lace la pamutu, kapena la pamphumi.

43 Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati cotupa cace ca nthenda ciri cotuuluka pa dazi la pa mutu wace, kapena la pamphumi pace, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;

44 ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amuchetu wodetsedwa; nthenda yace iri pamutu pace.

45 Ndipo azing'amba zobvala zace za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pace lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wace wa m'mwamba, napfuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!

46 Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pace pakhale kunja kwa cigono.

47 Ndiponso ngati nthenda yakhate iri pa cobvala caubweya, kapena cathonje;

48 ngakhale iri pamuyaro, kapena pamtsendero, cathonje, kapena caubweya, ngakhale iri pa cikopa, kapena pa cinthu ciri conse copanga ndi cikopa;

49 ngati nthenda iri yobiriwira, kapena yofiira pacobvala, kapena pacikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;

50 ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse ciija ca nthenda masiku asanu ndi awiri;

51 naone nthenda tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati nthenda yakula pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pacikopa, ziri zonse zanchito zopangika ndi cikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndico codetsedwa.

52 Ndipo atenthe cobvalaco ngakhale muyaro wace, ngakhale mtsendero wace, caubweya kapena cathonje, kapena ciri conse cacikopa ciri ndi khate, ndilo khate lofetsa; acitenrhe ndi mote.

53 Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pacobvala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa;

54 pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke cija pali khate, nacibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;

55 ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ace, yosakulanso nthenda, ndico codetsedwa; ucitenthe ndi moto; ndilo pfunka, kungakhale kuyera kwace kuli patsogolo kapena kumbuyo.

56 Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa cobvala, kapena cikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;

57 ndipo ikaonekabe pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, irikubukanso; ucitenthe ndi moto cija canthenda.

58 Ndipo ukatsuka cobvalaco, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ngati nthenda yalekapo pa cimeneco, acitsukenso kawiri, pamenepo ciri coyera.

59 Ici ndi cilamulo ca nthenda yakhate iri pa cobvala caubweya kapena cathonje, ngakhale pamuyare, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa; kucicha coyera kapena kucicha codetsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27