Levitiko 19 BL92

Malamulo ena osiyanasiyana

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.

3 Ali yense aopemai wace, ndi atate wace; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

4 Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5 Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.

6 Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwace muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lacitatu, muzikatentha ndi moto.

7 Akakadya konse tsiku tacitatu kali conyansa, kosabvomerezeka:

8 koma ali yense akudyako adzasenza mphulupulu yace, popeza waipsa copatulidwa ca Yehova; ndi munthuyo amsadze, kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

9 Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.

10 Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

11 Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.

12 Musamalumbira monama ndi kuchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

13 Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zace; mphotho yace ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.

14 Usamatemberera wogontha; usamaika cokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

15 Musamacita cisalungamo pakuwemza mlandu; usamabvomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.

16 Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

17 Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera ucimo cifukwa ca iye.

18 Usamabwezera cilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.

19 Muzisunga malemba anga, Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamabvala cobvala ca nsaru za mitundu iwiri zosokonezana.

20 Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.

21 Ndipo adze nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, ndiyo nkhosa yamphongo ikhale nsembe yoparamula.

22 Ndipo wansembe acite comtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yoparamula pamaso pa Yehova, cifukwa ca kucimwa adacimwaku; ndipo adzakhululukidwa cifukwa ca kucimwa kwace adacimwaku.

23 Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzalamitengo yamitundumitundu ikhale ya cakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.

24 Koma caka cacinai zipatso zace zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova.

25 Caka cacisanu muzidya zipatso zace, kuti zobala zace zikucurukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

26 Musamadya kanthu ndi mwazi wace; musamacita nyanga, kapena kuombeza ula.

27 Musamameta mduliro, kapena kusenga m'mphepete mwa ndebvu zanu,

28 Musamadziceka matupi anu cifukwa ca akufa, kapena kutema mpbini; Ine ndine Yehova.

29 Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumcititsa cigololo; lingadzale ndi cigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zocititsa manyazi.

30 Muzisunga masabata anga, ndi kucitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

31 Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

32 Pali aimvi uziwagwadira, nucitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; lnendine Yehova.

33 Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.

34 Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

35 Musamacita cisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wace, kulemera kwace, kapena kucuruka kwace.

36 Mukhale naco coyesera coona, miyeso yoona, era woona, bini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto.

37 Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwacita; Ine ndine Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27