Levitiko 25 BL92

Za caka copumula dziko

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata.

3 Zaka zisanu ndi cimodzi ubzale m'munda mwako, ndi zaka zisanu ndi cimodzi udzombole mphesa zako, ndi kuceka zipatso zace;

4 koma caka cacisanu ndi ciwiri cikhale sabata lakupumula la dziko, sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako.

5 Zophuka zokha zofikira masika usamazichera, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usaziceka; cikhale caka copumula dziko.

6 Ndipo sabata la dzikoli likhale kwa inu la cakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa nchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;

7 ndi ng'ombe zako, ndi nyama ziri m'dziko lako; zipatso zace zonse zikhale cakudya cao.

Za caka coliza lipenga

8 Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.

9 Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la citetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.

10 Ndipo mucipatule caka ca makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muciyese caka coliza lipenga; ndipo mubwerere munthu ali yense ku zace zace, ndipo mubwerere yense ku banja lace.

11 Muciyese caka ca makomi asanuco coliza lipenga, musamabzala, kapena kuceka zophuka zokha m'mwemo; kapenakuceka mphesa zace za mipesa yosadzombola.

12 Popeza ndico caka coliza lipenga; muciyese copatulika, mudye zipatso zace kunja kwa munda.

13 Caka coliza lipenga ici mubwerere nonse ku zace zace.

14 Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana;

15 monga mwa kuwerenga kwace kwa zaka, citapita coliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.

16 Monga mwa kucuruka kwa zaka zace uonjeze mtengo wace, ndi monga mwa kucepa kwa zaka zace ucepse mtengo wace; pakuti akugulitsa powerenga masiku ace.

17 Musamasautsana, koma uope Mulungu wako; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

18 M'mwemo mucite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita; ndipo mudzakhala m'dzikomo okhazikika.

19 Dziko lidzaperekanso zipatso zace, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi k'ukhalamo okhazikika.

20 Ndipo mukadzati, Tidzadyanji caka cacisanu ndi ciwiri? taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;

21 pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu caka cacisanu ndi cimodzi, ndipo cidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.

22 Ndipo mubzale caka cacisanu ndi citatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira caka cacisanu ndi cinai, mpaka zitacha zipatso zace mudzadya zasundwe.

Za kuombola dziko ndi nyumba

23 Ndipo asaligulitse dziko cigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.

24 Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.

25 Mbale wako akasaukira cuma, nakagulitsa cace cace, pamenepo mombolo wace, mbale wace weni weni azidza, naombole cimene mbale wace anagulitsaco.

26 Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lace lacionetsa, nacipeza cofikira kuciombola;

27 pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwace, nabwezere wosulayo zotsalirapo, nabwerere iye ku dziko lace.

28 Koma dzanja lace likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo cogulitsaco cikhale m'dzanja lace la iye adacigulayo, kufikira caka coliza lipenga; koma caka coliza lipenga cituruke, nabwerere iye ku dziko lace.

29 Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m'mudzi wa m'linga, aiombole cisanathe caka coigulitsa; kufikira kutha caka akhoza kuombola.

30 Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwace kwa caka camphumphu, nyumba iri m'mudzi wa m'lingayi idzakhala yace ya iye adaigula yosamcokeranso mwa mibadwo yace; siidzaturuka caka coliza lipenga.

31 Koma nyumba za m'midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m'dziko; ziomboledwe, zituruke m'caka coliza lipenga.

32 Kunena za midzi ya Alevi, nyumba za m'midzi yao yao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse.

33 Ndipo munthu akagula kwa Mlevi, nyumba yogulayo yokhala m'mudzi wace wace, ituruke m'caka coliza lipenga, popeza nyumba za m'midzi ya Alevi ndizo zao zao mwa ana a Israyeli.

34 Koma dambo la podyera pao siligulika; popeza ndilo lao lao kosatha.

35 Ndipo mbale wako akasaukira cuma, ndi dzanja lace lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.

36 Usamambwezetsa phindu, kapena cioniezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.

37 Musamampatsa ndarama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pocibwezera.

38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu.

Za mbale wodzigulitsa akhale kapolo

39 Ndipo mbale wako akasaukira cuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa nchito monga kapolo;

40 azikhala nawe ngati wolipidwa nchito, ngati munthu wokhala nawe; akutumikire kufikira caka coliza lipenga.

41 Pamenepo azituruka kukucokera, iye ndi ana ace omwe, nabwerere ku mbumba yace; abwerere ku dziko lao lao la makolo ace.

42 Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.

43 Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.

44 Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo amuna ndi akazi.

45 Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anu anu.

46 Ndipo muwayese colowa ca ana anu akudza m'mbuyo, akhale ao ao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israyeli, musamalamulirana mozunza.

47 Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera cuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa pfuko la banja la mlendo;

48 atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ace amuombole;

49 kapena mbale wa atate wace, kapena mwana wa mbale wa atate wace amuombole, kapena mbale wace ali yense wa banja lace amuombole; kapena akalemera cuma yekha adziombole yekha.

50 Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira caka adadzigulitsa kwa iye kufikira caka coliza lipenga; ndipo mtengo wace ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.

51 Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndarama zakumuombola zocokera ku ndalama zomgulazo.

52 Ndipo zikamtsalira zaka pang'ono kufikira caka coliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zace abwezere mtengo wace wakumuombola.

53 Akhale naye monga wolipidwa caka ndi caka; asamamlamulira momzunza pamaso pako,

54 Ndipo akapanda kumuombola motero, azituruka caka coliza lipenga, iye ndi ana ace omwe.

55 Pakuti ana a Israyeli ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27