Levitiko 23 BL92

Za nyengo zoikika za Yehova

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.

3 Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira nchito konse; ndilo sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.

Paskha

4 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, masonkhano opatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.

5 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, pali Paskha wa Yehova.

6 Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi womwewo ndilo madyerero a mkate wopanda cotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa.

7 Tsiku lace loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena.

8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lacisanu ndi ciwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.

Zipatso zoyamba

9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kuceka dzinthu zace, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;

11 ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata sabata wansembe aweyule.

12 Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonze mwana wa nkhosa wopanda cirema, wa caka cimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.

13 Ndipo nsembe yaufa yace ikhale awiri a magawo khumi a ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, icite pfungo lokoma; ndi nsembe yace yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.

14 Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza naco copereka ca Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.

15 Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wa nsembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;

16 muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lacisanu ndi ciwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.

17 Muturuke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi cotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.

18 Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, ana a nkhosa asanu ndi awiri, opanda cirema a caka cimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.

19 Mukonzenso mwana wa mbuzi mmodzi akhale nsembe yaucimo, ndi ana a nkhosa awiri a caka cimodzi akhale nsembe yoyamika.

20 Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi ana a nkhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.

21 Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.

22 Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

24 Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko cikumbutso ca kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.

25 Musamagwira nchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.

Tsiku la citetezero

26 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

27 Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wacisanu ndi ciwiri, ndilo tsiku la citetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzicepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.

28 Musamagwira nchito iri yonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la citetezero, kucita cotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29 Pakuti munthu ali yense wosadzicepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wace.

30 Ndi munthu ali yense wakugwira nchito iri yonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wace.

31 Musamagwira nchito iri yonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zoo nse.

32 Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzicepetse; tsiku lacisanu ndi cinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.

Madyerero a misasa

33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

34 Nena ndi ana a Israyeli, kuti, Tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi uno wacisanu ndi ciwiri pali madyerero a misasa a Yehova, masiku asanu ndi awiri.

35 Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira nchito ya masiku ena.

36 Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lacisanu ndi citatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira nchito ya masiku ena.

37 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lace lace;

38 pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zoo winda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.

39 Koma tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi ciwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lacisanu ndi citatu mupumule.

40 Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yobvalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri.

41 Ndipo muwasunge madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri m'caka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wacisanu ndi ciwiri.

42 Mukhale m'misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m'dziko mwa Israyeli akhale m'misasa;

43 kuti mibadwo yanu ikadziwe lruti ndinakhalitsa ana a Israyeli m'misasa, pamene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

44 Ndipo Mose anafotokozera ana a Israyeli nyengo zoikika za Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27