Levitiko 7 BL92

Cilamulo ca nsembe yo paramula

1 Ndipo cilamulo ca nsembe yoparamula ndi ici: ndiyo yopatulikitsa.

2 Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo aziphera nsembe yoparamula; nawaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

3 Ndipo acotseko, nabwere nao mafuta ace onse; mcira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,

4 ndi imso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso;

5 ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yoparamula.

6 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulikitsa.

7 Monga nsembe yaucimo, momwemo nsembe yoparamula; pa zonse ziwirizi pali cilamulo cimodzi; ikhale yace ya wansembeyo, amene acita nayo cotetezera.

8 Ndipo cikopa ca nsembe yopsereza cikhale cace cace ca wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu ali yense.

9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumcembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi paciwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo,

10 Ndipo nsembe zonse zaufa zosanganiza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.

Cilamulo ca nsembe yoyamika

11 Ndipo cilamulo ca nsembe zoyamika, zimene azibwera Daze kwa Yehova ndi ici:

12 akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndinsembe yolemekeza, timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tooca, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.

13 Abwere naco copereka cace pamodzi ndi timitanda ta mkate wacotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zace.

14 Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.

15 Kunena za nyama ya nsembe volemekeza ya nsembe zoyamika zace, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.

16 Koma nsembe ya copereka cace ikakhala ya cowinda, kapena copereka caufuhi, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yace; ndipo m'mawa adye cotsalirapo;

17 koma cotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lacitatu, acitenthe.

18 Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zace tsiku lacitatu, sikubvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo cinthu conyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zace.

19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kali konse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama yina, ali yense ayera aidyeko.

20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala naco comdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

21 Ndipo munthu akakhudza cinthu codetsa, codetsa ca munthu, kapena codetsa ca zoweta, kapena ciri conse conyansa codetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

Aletsedwa asadye mafuta ndi mwazi

22 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

23 Lankhula ndi ana a Israyeli ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng'ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.

24 Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi cirombo ayenera nchito iri yonse, koma musamadya awa konse konse.

25 Pakuti ali yense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

26 Ndipo musamadya mwazi uti wonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse,

27 Ali yense akadya mwazi uti wonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

Za gawo la ansembe

28 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

29 Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yace kwa Yehova, azidza naco copereka cace kwa Yehova cocokera ku nsembe yoyamika yace;

30 adze nazo m'manja mwace nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

31 Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo pa guwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Arent ndi ana ace.

32 Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe, ukhale nsembe yokweza yocokera ku nsembe zoyamika zanu.

33 Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lace la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera Ilao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.

34 Pakuti ndatengako kwa ana a Israyeli, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ace, zikhale zoyenera iwo kosatha zocokera kwa ana a Israyeli.

35 Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ace, locokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;

36 limene Yehova anauza ana a Israyeli aziwapatsa, tsiku limene iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.

37 Ico ndi cilamulo ca nsembe yopsereza, ca nsembe yaufa, ca nsembe yaucimo, ndi ca nsembe yoparamula, ndi ca kudzaza dzanja, ndi ca nsembe zoyamika;

38 cimene Yehova analamulira Mose m'phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israyeli abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m'cipululu ca Sinai.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27