Levitiko 20 BL92

Ziletsedwa cipembedzo ca Moleke ndi zoipa zina

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Unenenso kwa ana a Israyeli ndi kuti, Ali yense wa ana a Israyeli, kapena wa alendo akukhala m'Israyeli, amene apereka mbeu zace kwa Moleke, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.

3 Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace; popeza anapereka a mbeu zace kwa Moleke, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.

4 Ndipo ngati anthu a m'dzikomo akambisa munthuyo pang'ono ponse, pamene apereka a mbeu zace kwa Moleke, kuti asamuphe;

5 pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lace, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi cigololo kukacita cigololo kwa Moleke, kuwacotsa pakati pa anthu a mtundu wao.

6 Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi cigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace.

7 Cifukwa cace dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8 Ndipo musunge malemba anga ndi kuwacita; Ine ndine Yehova wakupatula inu.

9 Pakuti ali yense wakutemberera atate wace kapena mai wace azimupha ndithu; watemberera atate wace kapena mai wace; mwazi wace ukhale pamutu pace.

10 Munthu akacita cigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wacita cigololo ndi mkazi wa mnansi wace, awaphe nditho, mwamuna ndi mkazi onse awiri.

11 Munthu akagona naye mkazi wa atate wace, wabvula atate wace; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamtu pao.

12 Munthu akagona ndi mpongozi wace, awaphe onse awiri; acita cisokonezo; mwazi wao ukhale pamtu pao.

13 Munthu akagonana ndi mwamuna mnzace, monga amagonana ndi mkazi, acita conyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.

14 Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wace cocititsa manyazi ici; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale cocititsa manyazico pakati pa inu.

15 Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi.

16 Mkazi akasendera kwa nyama iri yonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.

17 Munthu akatenga mlongo wace, mwana wamkazi wa atate wace, kapena mwana wamkazi wa mai wace, nakaona thupi lace, ndi mlongoyo akaona thupi lace; cocititsa manyazi ici; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anabvula mlongo wace; asenze mphulupulu yace.

18 Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakambvula, anabvula kasupe wace, ndi iye mwini anabvula kasupe wa nthenda yace; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.

19 Usamabvula mbale wa mai wako, kapena mlongo wa atate wako; popeza anabvula abale ace; asenze mphulupulu yao.

20 Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wace, nabvula mbale wa atate wace; asenze kucimwa kwao; adzafa osaona ana.

21 Munthu akatenga mkazi wa mbale wace, codetsa ici; wabvula mbale wace; adzakhala osaona ana.

22 Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwacita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.

23 Musamatsata miyambo ya mtundu umene neliucotsa pamaso panu; popeza anacita izi zonse, nelinalema nao.

24 Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu yina ya anthu.

25 Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kali konse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.

26 Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.

27 Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27