Levitiko 14 BL92

Malamulo a pa kumyeretsa wakhate

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,

2 Cilamulo ca wakhate tsiku la kumyeretsa kwace ndi ici: azidza naye kwa wansembe;

3 ndipo wansembe aturuke kumka kunja kwa cigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda Yakhate yapola pa wakhateyo;

4 pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi, ubweya wofiira, ndi hisope;

5 ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;

6 natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;

7 nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lace, namuche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.

8 Ndipo iye wakutiayeretsedwe atsuke zobvala zace, namete tsitsi lace lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kucigono, koma agone pa bwalo la hema wace masiku asanu ndi awiri.

9 Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lace lonse la pamutu pace, ndi ndebvu zace, ndi nsidze zace, inde amete tsitsi lace lonse; natsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nakhale woyera.

10 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge ana a nkhosa awiri, amuna opanda cirema, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamkazi wa caka cimodzi wopanda cirema, ndi atatu a magawo khumi a ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa mafuta.

11 Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako;

12 ndipo wansembe atenge mwana wa nkhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yoparamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

13 Ndipo akaphere mwana wa nkhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yaucimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yaucimo momwemo nsembe yoparamula, nja wansembe; ndiyo yopatulikitsa.

14 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;

15 ndipo wansembe atengeko muyeso wa mafuta, nawathire pa cikhato ca dzanja lace lamanzere la iye mwini;

16 ndipo wansembe abviike cala cace ca dzanja lace lamanja ca iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lace lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi cala cace pamaso pa Yehova;

17 ndipo wansembe apakeko mafuta okh a ria m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yoparamula;

18 natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lace la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amcitire comtetezers pamaso pa Yehova.

19 Ndipo wansembe apereke nsembe yaucimo, namcitire comtetezera amene akuti ayeretsedwe, cifukwa ca kudetsedwa kwace; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;

20 ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa pa guwa la nsembe; ndipo wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.

21 Ndipo akakhala waumphawi cosafikana cuma cace azitenga mwana wa nkhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yoparamula, aiweyule kumcitira comtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi wa mafuta;

22 ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yaucimo, ndi linzace la nsembe yopsereza.

23 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la cihema cokomanako, pamaso pa Yehova.

24 Ndipo wansembe atenge mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndi muyeso wa mafuta, ndipo wansembe aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;

25 naphe mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;

26 ndipo wansembe athireko mafuta aja m'cikhato cace camanzere ca iye mwini;

27 ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lace lamanzere ndi cala cace ca dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;

28 ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca: dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa usembe yoparamula;

29 ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumcitira comtetezera pamaso pa Yehova.

30 Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo, limodzi la nsembe yaucimo, ndi tina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa;

31 ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova.

32 Ici ndi cilamulo ca iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pace.

33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

34 Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanu lanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanu lanu;

35 pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.

36 Ndipo wansembe aziuza kuti aturutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse ziri m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;

37 naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ace yakumba kubzola khoma;

38 pamenepo wansembe azituruka ku khomo la nyumba, natseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri;

39 ndipo wansembe abwerenso tsiku lacisanu ndi ciwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba;

40 pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mudzi;

41 napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

42 natenge miyala yina, naikhazike m'male mwa miyala ija; natenge dothi tina, namatenso nyumbayo.

43 Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso;

44 pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.

45 Ndipo apasule nyumbayo, miyala yace, ndi mitengo yace, ndi dothi lace lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda.

46 Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ace iriyotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

47 Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zobvala zace; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zobvala zace.

48 Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aiche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.

49 Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;

50 naphe mbalame imodzi m'mbale yadothi, pamwamba pa madzi oyenda;

51 natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, nazibviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;

52 nayeretsenyumbandi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.

53 Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aicitire coitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.

54 Ici ndi cilamulo ca nthenda iri yonse yakhate, ndi yamfundu;

55 ndi ya khate la cobvala, ndi la nyumba;

56 ndi yacotupa, ndi yankhanambo, ndi yacikanga;

57 kulangiza tsiku loti cikhala codetsa, ndi tsiku loti cikhala coyera; ici ndi cilamulo ca khate.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27