Levitiko 4 BL92

Za nsembe yaucimo pocimwa wansembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Munthu akacimwa, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Mulungu, nakacitapo kanthu;

3 akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kuparamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita, ikhale nsembe yaucimo.

4 Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la cihema cokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lace pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

5 Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwerenao ku cihema cokomanako;

6 ndipo wansembeyo abviike cala cace m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova cakuno ca nsaru yocinga, ya malo opatulika.

7 Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la cofukiza ca pfungo lokoma, lokhala m'cihema cokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.

8 Ndipo acotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yaucimo, acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

9 ndi imso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso,

10 umo azikacotsera pa ng'ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe yopsereza.

11 Naturutse cikopa ca ng'ombeyo, ndi nyama yace yonse, pamodzi ndi mutu wace, ndi miyendo yace, ndi matumbo ace, ndi cipwidza cace,

12 inde ng'ombe yonse, kunja kwa cigono, kumka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.

Za nsembe yaucimo pocimwa mtundu wonse wa lsrayeli

13 Ndipo khamu lonse la Israyeli likalakwa osati dala, ndipo cikabisika cinthuci pamaso pa msonkhano, litacita cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, ndi kuparamula;

14 kukadziwika kucimwa adacimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yaucimo, ndipo udze nayo ku khomo la cihema cokomanako.

15 Ndipo akuru a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

16 Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng'ombeyo ku cihema cokomanako;

17 nabviike cala cace m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, cakuno ca nsaru yocinga.

18 Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'cihema cokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.

19 Ndipo acotse mafuta ace onse, nawatenthe pa guwa la nsembe.

20 Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anacitira ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo wansembe awacitire cowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21 Ndipo aturutse ng'ombeyo kunja kwa cigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yaucimo ya kwa msonkhano.

Za nsembe yaucimo pocimwa mkuru

22 Akacimwa mkuru, osati dala, pa cina ca zinthu ziti zonse aziletsa Yehova Mulungu wace, naparamula;

23 akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace, ndico tonde wopanda cirema;

24 naike dzanja lace pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.

25 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.

26 Ndipo atenthe mafuta ace onse pa guwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

Za nsembe yaucimo pocimwa munthu yekha

27 Ndipo akacimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, naparamula;

28 akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita.

29 Aike dzanja lace pamutu pa nsembe yaucimo, naiphe nsembe yaucimo pamalo pa nsembe yopsereza.

30 Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe.

31 Nacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

32 Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo copereka cace, ikhale nsembe yaucimo, azidza nayo yaikazi, yopanda cirema.

33 Naike dzanja lace pa mutu wa nsembe yaucimo, ndi kuipha ikhale nsembe yaucimo pamalo pophera nsembe yopsereza.

34 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe;

35 nawacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe, awa pa guwa la nsembe, monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pa kucimwa kwace adakucimwira, ndipo adzakhululukidwa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27