Levitiko 6 BL92

Za nsembe yoparamula pocimwa dala munthu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Akacimwa munthu nakacita mosakhulupirika pa Yehova nakacita monyenga ndi mnansi wace kunenaza coikiza, kapena cikole, kapena cifwamba, kapena anasautsa mnansi wace;

3 kapena anapeza cinthu cotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa cimodzi ca izi zonse amacita munthu, ndi kucimwapo;

4 pamenepo padzali kuti popeza anacimwa, naparamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwacifwamba, kapena cinthuci adaciona ndi kusautsa mnzace, kapena coikiza anamuikiza, kapena cinthu cotayika anacipeza;

5 kapena ciri conse analumbirapo monama; acibwezere conseci, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ici kwa mwini wace tsiku lotsutsidwa iye.

6 Ndipo adze nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola mwace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula, adze nayo kwa wansembe;

7 ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena ziti zonse akazicita ndi kuparamula nazo.

Cilamulo ca nsembe yopsereza

8 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

9 Uza Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Cilamulo ca nsembe yopsereza ndi ici: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za pa guwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo mota wa pa guwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

10 Ndipo wansembe abvale mwinjiro wace wabafuta, nabvale pathupi pace zobvala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, mota utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.

11 Pamenepo abvule zobvala zace, nabvale zobvala zina, nacotse phulusa kumka nalo kunja kwa cigono, kumalo koyera.

12 Ndipo mota wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.

13 Moto uziyakabe pa guwa la nsembe, wosazima.

Cilamulo ca nsembe yaufa

14 Ndipo cilamulo ca copereka caufa ndico: ana a Aroni azibwera naco pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.

15 Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa copereka ca ufa wosalala, ndi pa mafuta ace, ndi libona lonse liri pa copereka caufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zicite pfungo lokoma, ndizo cikumbutso cace ca kwa Yehova.

16 Ndipo cotsalira cace adye Aroni ndi ana ace; acidye copanda cotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la cihema cokomanako acidye.

17 Asaciphike ndi cotupitsa, Ndacipereka cikhale gawo lao locokera pa nsembe zanga zamoto; ndico copatulikitsa, monga nsembe yaucimo, ndi monga nsembe yoparamula.

18 Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, ciwacokere ku nsembe zamoto za Yehova; ali yense wakuzikhudza izi adzakhala wapatolika.

Nsembe ya ansembe podzozedwa iwo

19 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

20 Copereka ca Aroni ndi ana ace, cimene azibwera naco kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ici: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale copereka caufa kosalekeza, nusu lace m'mawa, nusu lace madzulo.

21 Cikonzeke paciwaya ndi mafuta; udze naco cokazinga; copereka caufa cazidutsu ubwere naco, cikhale pfungo lokoma la kwa Yehova.

22 Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwace, wa mwa ana ace, acite ici; likhale lemba losatha; acitenthe konse kwa Yehova.

23 Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.

Cilamulo ca nsembe yaucimo

24 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

25 Lankhula ndi Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Cilamulo ca nsembe yaucimo ndi ici: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yaucimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulikitsa.

26 Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka cifukwa ca zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la cihema cokomanako.

27 Ali yense akakhudza nyama yace adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wace wina pa cobvala ciri conse, utsuke cimene adauwazaco m'malo opatulika.

28 Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi.

29 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulikitsa.

30 Koma asadye nsembe yaucimo iri yonse, imene amadza nao mwazi wace ku cihema cokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27