1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao,
2 Nenani ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse ziri pa dziko lapansi.
3 Nyama iri yonse yogawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.
4 Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda; ngamila, angakhale abzikula, koma yosagawanika ciboda, muziiyesa yodetsedwa.
5 Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika ciboda, muiyese yodetsedwa.
6 Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika ciboda, mumuyese wodetsedwa.
7 Ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.
8 Nyama yace musamaidya, mitembo yace musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.
9 Mwa zonse ziri m'madzi muyenera kumadya izi: ziri zonse ziti nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.
10 Koma ziti zonse ziribe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse ziri m'madzi, muziziyesa zonyansa;
11 inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.
12 Ziri zonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa.
13 Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; siziyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi;
14 ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wace;
15 kungubwi mwa mtundu wace;
16 ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi mwa mtundu wace;
17 ndi nkhutunkhutu ndi nswankhono ndi mancici;
18 tsekwe, bvuwo, ndi dembu;
19 indwa, ndi cimeza monga mwa mtundu wace, ndi sadzu, ndi mleme.
20 Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa,
21 Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kuthumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:
22 dzombe mwa mtundu wace, ndi cirimamine mwa mitundu yace, ndi njenjete mwa mtundu wace ndi tsokonombwe mwa mitundu yace.
23 Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa.
24 Ndipo izi zikudetsani: ali yense akhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;
25 ndipo ali yense akanyamulako nyama ya mtembo wace azitsuka zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
26 Nyama iri yonse yakugawanika ciboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; ali yense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.
27 Ndipo iri yonse iyenda yopanda ciboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; ali yense wokhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28 Ndipo iye amene akanyamula mtembo wace atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.
29 Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wace;
30 ndi gondwa, ndi mng'anzi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi mfuko.
31 Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; ali yense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
32 Ndipo ciri conse cakufa ca izi cikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale cipangizo camtengo, kapena cobvala, kapena cikopa kapena thumba, cipangizo ciri conse cimene agwira naco nchito, acibviike m'madzi, ndipo cidzakhala codetsedwa kufikira madzulo; pamenepo cidzakhala coyera.
33 Ndipo ciri conse ca izi cikagwa m'cotengera ciri conse cadothi, cinthu cokhala m'mwemo cidetsedwa, ndi cotengeraco muciswe.
34 Cakudya ciri conse cokhala m'mwemo, cokonzeka ndi madzi, cidzakhala codetsedwa; ndi cakumwa ciri conse m'cotengera cotere cidzakhala codetsedwa.
35 Ndipo kanthu ka mtembo wace kakagwa pa zinthu ziri zonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mcembo kapena mphika wobvundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.
36 Koma kasupe kapena citsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa.
37 Ndipo kanthu ka mtembo wace kakagwa pa mbeu yofesa, ikati ifesedwe, idzakhala yoyera.
38 Koma akathira madzi pa mbeuyi, ndi kanthu ka mtembo wace kakagwapo, muiyese yodetsedwa.
39 Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
40 Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wace azitsuka zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wace atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
41 Ndipozokwawazonsezakukwawa pa dziko lapansi zikhale zonyansa; musamazidya.
42 Zonse zoyenda cafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa.
43 Musamadzinyansitsa ndi cokwawa ciri conse cakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo.
44 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi cokwawa ciri conse cakukwawa pansi.
45 Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndikhale Mulungu wanu; cifukwa cace mukhale oyera, popeza ine ndine woyera.
46 Ici ndi cilamulo ca nyama, ndi ca mbalame, ndi ca zamoyo zonse zakuyenda m'madzi, ndi ca zamoyo zonse zakukwawa pansi;
47 kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.