Levitiko 26 BL92

Malamulo, malonjezo, ndi macenjezo

1 Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena coimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

2 Musunge masabata anga, ndi kucitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

3 Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita;

4 ndidzakupatsani mvula m'nyengo zace, ndi dziko lidzapereka zipatso zace, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zace.

5 Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yochera mphesa, ndi nyengo yochera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta naco cakudya canu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.

6 Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zirombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.

7 Mudzapitikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga,

8 Asanu ainu adzapitikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapitikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

9 Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukucurukitsani; ndipo ndidzakhazika cipangano canga ndinapangana nanuco.

10 Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kuturutsa zakale cifukwa ca zatsopano.

11 Ndidzamanga kacisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.

12 Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.

13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinatyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani coweramuka.

14 Koma mukapanda kundimvera Ine, osacita malamulo awa onse;

15 ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzacita malamulo anga onse, koma kutyola cipangano canga;

16 ndidzacitira inu icinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthendayoondetsayam'cifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu cabe, pope za adani anu adzazidya.

17 Ndipt nkhope yanga idzatsutsana nanu kuti adani anu adzakukanthani, ndipt akudana ndi inu adzacita ufumu Pl inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.

18 Ndipo muka panda kundimvera, zingakhale izi ndidzaonjeza kukulangani kasanu nd kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.

19 Popeza ndidzatyola mphamvu yam yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati citsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;

20 ndipo mudzacita nayo mphamvu yanu cabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatse zace, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zace.

21 Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zocimwa zanu.

22 Popeza ndidzatumiza cirombo ca kuthengo pakati pa inu, ndipo cidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nicidzacepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.

23 Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;

24 Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zoipa zanu.

25 Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakucita cilango ca cipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.

26 Pamene ndityola mcirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mcembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.

27 Ndipo mukapanda kundimvera Ine, cingakhale ici, ndi kuyenda motsutsana nane;

28 Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.

29 Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.

30 Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31 Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za pfungo lanu lokoma.

32 Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.

33 Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja.

34 Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ace, masiku onse a kupasuka kwace, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ace.

35 Masiku onse a kupasuka kwace lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo.

36 Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapitikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.

37 Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.

38 Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.

39 Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.

40 Pamenepo adzabvomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pocita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,

41 Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzicepetsa, ndipo abvomereza kulanga kwa mphulupulu zao;

42 pamenepo ndidzakumbukila pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isake, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukila; ndipo ndidzakumbukila dzikoli.

43 Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ace, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzabvomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.

44 Ndiponso pali icinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kutyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Muhmgu wao.

45 Koma cifukwa ca iwo ndidzawakumbukila pangano la makolo ao, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.

46 Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa iye ndi ana a Israyeli m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27