Levitiko 18 BL92

Malamulo a pa ulemu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Ine ndine Yehova Molungu wanu.

3 Musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Aigupto muja munakhalamo; musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.

4 Muzicita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5 Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawacita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

6 Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wacekumbvula; Ine ndine Yehova.

7 Usamabvula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamambvula.

8 Usamabvula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.

9 Usamabvula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.

10 Usamabvula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.

11 Usamabvula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.

12 Usamabvula mlongo wa atate wako; ndiye wa cibale ca atate wako.

13 Usamabvula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako.

14 Usamabvula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wace; ndiye mai wako.

15 Usamabvula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamambvula.

16 Usamabvula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako.

17 Usamabvula mkazi ndi mwana wamkazi wace; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wace, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wace kumbvula; ndiwo abale; cocititsa manyazi ici.

18 Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wace, kumbvuta, kumbvula pamodzi ndi mnzace, akah ndi moyo mnzaceyo.

19 Usamasendera kwa mkazi kumbvula pokhala ali padera cifukwa ca kudetsedwa kwace.

20 Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

21 Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto cifukwa ca Moleke, usamaipsa dzina la Mulungu wako: Ine ndine Yehova.

22 Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; conyansa ici.

23 Ndipo usamagonana ndi nyama iri yonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; cisokonezo coopsa ici.

24 Musamadzidetsa naco cimodzi ca izi; pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;

25 dziko lomwe lidetsedwa; cifukwa cace ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo.

26 Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osacita cimodzi conse ca zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu;

27 (pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazicita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa)

28 lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.

29 Pakuti ali yense akacita ciri conse ca zonyansa Izi, inde amene azicita idzasadzidwa pakati pa anthu a mtundu wao.

30 Potero muzisunga cilangizo canga, ndi kusacita ziri zonse za miyambo yonyansayi anaicita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu-wako.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27