1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana amuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira;
2 ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsaru yocinga, pali cotetezerapo cokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pacotetezerapo.
3 Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.
4 Abvale maraya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zobvala za kumiyendo pathupi pace, nadzimangire m'cuuno ndi mpango wabafuta, nabvale nduwira yabafuta; izi ndi zobvala zopatulika; potero asambe thupi lace ndi madzi, ndi kubvala izi.
5 Ndipo ku khama la ana a Israyeli atenge atonde awiri akhale a nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.
6 Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndiyo yace yace, nacite codzitetezera iye yekha, ndi mbumba yace.
7 Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pa cihema cokomanako.
8 Ndipo Aroniayesemaere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli.
9 Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yaucimo.
10 Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.
11 Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndiyo yace yace, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yace, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yaucimo ndiyo yace yace;
12 natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makara amoto, kuwacotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ace odzala ndi cofukiza copera ca pfungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsaru yocinga;
13 naike cofukizaco pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa cofukiza ciphimbe cotetezerapo cokhala pamboni, kuti angafe.
14 Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi cala cace pacotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi cala cace cakuno ca cotetezerapo kasanu ndi kawiri.
15 Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yaucimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wace m'tseri mwa nsaru yocinga, nacite nao mwazi wace monga umo anacitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pacotetezerapo ndi cakuno ca cotetezerapo;
16 nacitire cotetezera malo opatulika, cifukwa ca kudetsedwa kwa ana a Israyeli, ndi cifukwa ca zolakwa zao, monga mwa zocimwa zao zonse; nacitire cihema cokomanako momwemo, cakukhala nao pakati pa zodetsa zao.
17 Ndipo musakhale munthu m'cihema cokomanako pakulowa iye kucita cotetezera m'malo opatulika, kufikira aturuka, atacita cotetezera yekha, ndi mbumba yace, ndi msonkhano wonse wa Israyeli.
18 Ndipo aturukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulicitira cotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.
19 Ndipo awazepo mwazi wina ndi cala cace kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulicotsera zodetsa za ana a Israyeli.
20 Ndipo atatha kucitira cotetezera malo opatulika, ndi cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;
21 ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,
22 ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m'cipululu.
23 Pamenepo Aroni alowe m'cihema cokomanako, nabvule zobvala zabafuta zimene anazibvala polowa m'malo opatulika, nazisiye komweko.
24 Ndipo asambe thupi lace ndi madzi kumalo kopatulika, nabvale zobvala zace, naturuke, napereke nsembe yopsereza yace, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nacite codzitetezera yekha ndi anthu.
25 Ndipo atenthe mafuta a nsembe yaucimo pa guwa la nsembe.
26 Ndipo iye amene anacotsa mbuzi ipite kwa Azazeli atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.
27 Koma ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndi mbuzi ya nsembe yaucimo, zimene mwazi wao analowa nao kucita nao cotetezera m'malo opatulika, aturuke nazo kunja kwa cigono; natenthe ndi mota zikopa zao, ndi nyama zao, ndi cipwidza cao.
28 Ndi iye amene anazitentha atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.
29 Ndipo lizikhala kwa Inu lemba Ilosatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira Debito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;
30 popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.
31 Likhale kwa inu sabata lakupumula, kuti mudzicepetse; ndilo lemba losatha.
32 Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lace acite nchito ya nsembe m'malo mwa atate wace, acite cotetezera, atabvala zobvala zabafuta, zobvala zopatulikazo.
33 Ndipo acite cotetezera malo opatulikatu, natetezere cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo.
34 Ndipo ici cikhale kwa inu lemba losatha, kucita cotetezera ana a Israyeli, cifukwa ca zocimwa zao zonse, kamodzi caka cimodzi. Ndipo anacita monga Yehova adauza Mose.