Levitiko 5 BL92

Za nsembe yoparamula

1 Ndipo akacimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osaulula, azisenza mphulupulu yace;

2 kapena munthu akakhudza ciri conse codetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa coweta codetsa, kapena mtembo wa cokwawa codetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi woparamula.

3 Kapena akakhudza codetsa ca munthu, ndico codetsa ciri conse akakhala codetsedwa naco, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula:

4 kapena munthu akalumbira ndi milomo yace osalingirira kucita coipa, kapena kucita cabwino, ciri conse munthu akalumbira osalingirira, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula cimodzi ca izi:

5 ndipo kudzali, ataparamula cimodzi ca izi, aziulula cimene adacimwa naco;

6 nadze nayo nsembe yoparamula kwa Yehova cifukwa ca kulakwa kwace adacimwira, ndiyo msoti wa nkhosa, kapena msoti wa mbuzi, ukhale nsembe yaucimo; ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace.

7 Ndipo cuma cace cikapanda kufikira nkhosa, wocimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yace yoparamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yaucimo, ndi yina ya nsembe yopsereza.

8 Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yaucimo, napotole mutu wace pakhosi pace, osaucotsa;

9 nawazeko mwazi wa nsembe yaucimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yaucimo.

10 Ndipo aikonze inzace ikhale nsembe yopsereza, manga mwa lemba lace; ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa adacimwira, ndipo adzakhululukidwa.

11 Koma cuma cace cikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wocimwayo azidza naco copereka cace limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yaucima; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo libona ai; pakuti ndico nsembe yaucimo.

12 Ndipo adze naco kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.

13 Ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace adacimwira cimodzi ca izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo cotsalira cikhale ca wansembe, monga umo amacitira copereka caufaco.

14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

15 Munthu akacita mosakhulupirika, nakacimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema, ya m'gulu lace, monga umayesa mtengo wace pochula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yoparamula;

16 ndipo abwezere colakwira copatulikaco, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amcitire comtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yoparamula; ndipo adzakhululukidwa.

17 Ndipo munthu akacimwa, nakacita dna ca zinthu ziti zonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma waparamula, azisenza mphulupulu yace.

18 Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola lace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula; ndipo wansembeyo amcitire comtetezera cifukwa ca kusacimwa dala kwace, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.

19 Iyo ndiyo nsembe yoparamula; munthuyu anaparamula ndithu pamaso pa Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27