Levitiko 9 BL92

Aroni adziperekera yekha ndi anthu nsembe, ndizo nsembe zoyamba

1 Ndipo kunali, tsiku lacisanu ndi citatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ace amuna, ndi akuru a Israyeli;

2 ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwana wa ng'ombe wamwamuna, akhale nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda cirema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.

3 Nunene kwa ana a Israyeli, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yaucimo; ndi mwana wa ng'ombe, ndi mwana wa nkhosa, a caka cimodzi, opanda cirema, akhale nsembe yopsereza;

4 ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.

5 Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa cihema cokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova,

6 Ndipo Mose anati, Ici ndi cimene Yehova anakuuzani kuti mucicite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

7 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yaucimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzicitire wekha ndi anthuwo cotetetezera; nupereke coperekaca anthu, ndi kuwacitira cotetezera; monga Yehova anauza.

8 Pamenepo Aroni anasendera kufupi kwa guwa la nsembe, napha mwana wa ng'ombe wa nsembe yaucimo, ndiyo ya kwa iye yekha.

9 Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anabviika cala cace m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde pa guwa la nsembe;

10 koma mafutawo, ndi imso, ndi cokuta ca mphafa za nsembe yaucimo, anazitentha pa guwa la nsembe; monga Yehova anauza Mose.

11 Ndipo anatentha ndi moto nyamayi ndi cikopa kunja kwa cigono.

12 Ndipo anapha nsembe yopsereza; ndi ana a Aroni anapereka mwaziwo kwa iye, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozu ngulira.

13 Ndipo anapereka nsembe yopsereza kwa iye, ciwalo ciwalo, ndi mutu wace; ndipo anazitentha pa guwa la nsembe.

14 Ndipo anatsuka matumbo ndi miyendo, nazitentha pa nsembe yopsereza pa guwa la nsembe.

15 Ndipo anabwera naco copereka ca anthu, natenga mbuzi ya nsembe yaucimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yaucimo, monga yoyamba ija.

16 Ndipo anabwera nayo nsembe yopsereza naipereka monga mwa lemba lace.

17 Ndipo anabwera nayo nsembe yaufa, natengako wodzala dzanja, nautentha pa guwa la nsembe, angakhale adatentha nsembe yopsereza ya m'mawa.

18 Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira, ndi mafuta a ng'ombe;

19 ndi a nkhosa, ndi mcira wamafuta, ndi cophimba matumbo, ndi imso, ndi cokuta ca mphafa;

20 ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo pa guwa la nsembe.

21 Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga iye anauza Mose.

22 Ndipo Aroni anakweza dzanja lace kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yaucimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika.

23 Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku cihema cokomanako, naturuka, nadalitsa anthu; ndipo ulemero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.

24 Ndipo unaturuka mota pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta pa guwa la nsembe; ndipo pakuciona anthu onse anapfuula, nagwa nkhope zao pansi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27