1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu cifukwa ca wakufa mwa anthu a mtundu wace;
2 koma cifukwa ca abale ace eni eni ndiwo, mai wace, ndi atate wace, ndi mwana wace wamwamuna, ndi mwana wace wamkazi, ndi mbale wace;
3 ndi cifukwa ca mlongo wace weni weni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse cifukwa ca iwowa.
4 Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wace, asadzidetse, ndi kudziipsa,
5 Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kucecerera ndebvu zao, kapena kudziceka matupi ao.
6 Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; cifukwa cace akhale opatulika.
7 Asadzitengere mkazi wacigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamcotsa mwamuna wace; popeza apatulikira Mulungu wace.
8 Cifukwa cace umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera,
9 Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kucita cigololo, alikuipsa atate wace; amtenthe ndi moto.
10 Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ace, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pace, amene anamdzaza dzanja kuti abvale zobvalazo, asawinde, kapena kung'amba zobvala zace.
11 Asafike kuli mtembo; asadzidetse cifukwa ca atate wace, kapena mai wace.
12 Asaturuke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wace; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wace ali pa iye; Ine ndine Yehova.
13 Ndipo adzitengere mkazi akali namwali.
14 Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wacigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wace akhale mkazi wace.
15 Asaipse mbeu yace mwa anthu a mtundu wace; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.
16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17 Nena ndi Aroni, kuti, Ali yense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala naco cirema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wace.
18 Pakuti munthu ali yense wokhala naco cirema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mph uno, kapena wamkuru ciwalo,
19 kapena munthu wopunduka phazi kapena wopunduka dzanja,
20 kapena wowerama, kapena wamfupi msinkhu, kapena wopunduka diso, kapena munthu wamphere, kapena wacipere, kapena wopunduka kumoto.
21 Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala naco cirema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali naco cirema asayandikize kupereka cakudya ca Mulungu wace.
22 Adye cakudya ca Mulungu wace, copatulikitsa, ndi copatulika;
23 koma asafike ku nsaru yocinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali naco cirema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.
24 Momwemo Mose ananena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana onse a Israyeli.