1 Pamene Yehova Mulungu wanu ataononga amitundu, amene Yehova Mulungu wanu akupatsani dziko lao, ndipo mutalilandira lanu lanu, ndi kukhala m'midzi mwao, ndi m'nyumba zao;
2 pamenepo mudzipatulire midzi itatu pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.
3 Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko.
4 Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzace wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzace osati dala, osamuda kale lonse;
5 monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzace kutema mitengo, ndi dzanja lace liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguruka m'mpinimo, nikomana ndi mnzace, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo;
6 kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzace, pokhala mtima wace watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanaparamula imfa, poona sanamuda kale lonse.
7 Cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire midzi itatu.
8 Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;
9 ukadzasunga lamulo ili lonse kulicita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace masiku onse; pamenepo mudzionjezere midzi itatu yina pamodzi ndi itatu iyi;
10 kuti angakhetse mwazi wosacimwa pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu, pangakhale mwazi pa inu.
11 Koma munthu akamuda mnzace, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkanth a moyo wace, kuti wafa; nakathawira ku wina wa midzi iyi;
12 pamenepo akuru a mudzi wace atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.
13 Diso lanu lisamcitire cifundo, koma mucotse mwazi wosacimwa m'Israyeli, kuti cikukomereni.
14 Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'colowa canu mudzalandiraci, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.
15 Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iri yonse, kapena cimo liri lonse adalicimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.
16 Mboni yaciwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa;
17 pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m'masiku awa;
18 ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wace;
19 mumcitire monga iye anayesa kumcitira mbale wace; motero mucotse coipaco pakati panu.
20 Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusacitanso monga coipaco pakati panu.
21 Ndipo diso lanu lisacite cifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.