Deuteronomo 24 BL92

Za kalata wa cilekaniro, cikole, kuba munthu, khate

1 Munthu akatenga mkazi akhale wace, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pace, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, ndi kumturutsa m'nyumba mwace.

2 Ndipo ataturuka m'nyumba mwace, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina.

3 Ndipo akamuda mwamuna waciwiriyo, nakamlemberanso kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, nakamturutsa m'nyumba mwace; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wace;

4 pamenepo mwamuna woyamba anamcotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wace, atadetsedwa iye; pakuti ici ndi conyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamacimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colandira canu.

5 Munthu akatenga mkazi watsopano, asaturuke nayo nkhondo, kapena asamcititse kanthu kali konse; akhale waufulu ku nyumba yace caka cimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.

6 Munthu asalandire cikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo cikole moyo wamunthu.

7 Akampeza munthu waba mbale wace wina wa ana a Israyeli, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzicotsa coipaco pakati panu.

8 Cenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kucita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kucita.

9 Kumbukilani cimene Yehova Mulungu wanu anacitira Miriamu panjira, poturuka inu m'dziko la Aigupto.

Za kukongoletsa

10 Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iri yonse, musamalowa m'nyumba mwace kudzitengera cikole cace.

11 Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituruka naco cikoleco kwa inu muli pabwalo.

12 Ndipo akakhala munthu waumphawi musagone muli naco cikole cace;

13 polowa dzuwa mumbwezeretu cikoleco, kuti agone m'cobvala cace, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani cilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Za cifundo pa anchito aumphawi, alendo ndi amasiye

14 Musamasautsa wolembedwa nchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu.

15 Pa tsiku lace muzimpatsa kulipira kwace, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wace ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhaireni cimo.

16 Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere cimo lace lace.

17 Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga cikole cobvala ca mkazi wamasiye;

18 koma muzikumbukila kuti munali akapolo m'Aigupto, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; cifukwa cace ndikuuzani kucita cinthu ici.

19 Mutasenga dzinthuzanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'nchito zonse za manja anu.

20 Mutagwedeza mtengo wanu wa azitona musayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye.

21 Mutachera m'munda wanu wamphesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye.

22 Ndipo muzikumbukila kuti munali: akapolo m'dziko la Aigupto; cifukwa cace ndikuuzani kucita cinthu ici.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34