1 Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwacangu, ndi kusamalira kucita malamulo ace onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;
2 ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
3 Mudzakhala odala m'mudzi, ndi odala kubwalo.
4 Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
5 Zidzakhala zodala mtanga wanu, ndi coumbiramo mkate wanu.
6 Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala poturuka inu.
7 Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.
8 Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse muturutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani,
9 Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace.
10 Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akuchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.
11 Ndipo Yehova adzakucurukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo,
12 Yehova adzakutsegulirani cuma cace cokoma, ndico thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yace, ndi kudalitsa nchito zonae za dzanja lanu; ndipo mudza kongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
13 Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mcira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwacita;
14 osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu yina kuitumikira.
15 Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,
16 Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo.
17 Zidzakhala zotembereredwa mtanga wanu ndi coumbiramo mkate wanu.
18 Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
19 Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa poturuka inu.
20 Yehova adzakutumizirani temberero, cisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukaturutsa dzanja lanu kucita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika rosanga, cifukwa ca zocita inu zoipa, zimene wandisiya nazo,
21 Yehova adzakumamatiritsani mliri kufikira akakuthani kukucotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.
22 Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya cifuwa, ndi malungo, ndi cibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, cinsikwi ndi cinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.
23 Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko liri pansi panu ngati citsulo.
24 Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale pfumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kucokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.
25 Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawaturukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
26 Ndipo mitembo yanu idzakhalacakudya ca mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zirombo zonse za pa dziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.
27 Yehova adzakukanthani ndi zirombo za ku Aigupto, ndi nthenda yoturuka mudzi, ndi cipere, ndi mphere, osacira nazo.
28 Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima;
29 ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.
30 Mudzaparana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzanka munda wamphesa, osalawa zipatso zace.
31 Adzapha ng'ombe yanu pamaso panu, osadyako inu; adzalanda buru wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.
32 Adzapereka ana anu amuna ndi akazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.
33 Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi nchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;
34 nimudzakhala oyeruka cifukwa comwe muciona ndi maso anu,
35 Yehova adzakukanthani ndi cironda coipa cosacira naco kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu.
36 Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu yina ya mitengo ndi miyala.
37 Ndipo mudzakhala codabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.
38 Mudzaturuka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.
39 Mudzanka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wace, kapena kuchera mphesa zace, popeza citsenda cidzaidya.
40 Mudzakhala nayo mitengo yaazitona m'malire anu onset osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo yaazitona zidzapululuka.
41 Mudzabala ana amuna ndi akazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.
42 Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zao zao za dzombe.
43 Mlendo wokhala pakati panu adzakulira-kulira inu, koma inu mudzacepera-cepera.
44 Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mcira.
45 Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace ndi malemba ace amene anakulamulirani;
46 ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati cizindikilo ndi cozizwa, nthawi zonse.
47 Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi cimwemwe ndi mokondwera mtima, cifukwa ca kucuruka zinthu zonse;
48 cifukwa cace mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lacitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.
49 Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wocokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;
50 mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamcitira cifundo mwana;
51 ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.
52 Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
53 Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.
54 Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu diso lace lidzaipira mbale wace, ndi mkazi wa pa mtima wace, ndi ana ace otsalira;
55 osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ace alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse.
56 Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lace popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lace lidzamuipira mwamuna wa pamtima pace, ndi mwana wace wamwamuna ndi wamkazi;
57 ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.
58 Mukapanda kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo YEHOVA MULUNGU ANU;
59 Yehova adzacita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwiza, miliri yaikuru ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.
60 Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Aigupto, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.
61 Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la cilamulo ici, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.
62 Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mukacuruka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
63 Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukucitirani zabwino, ndi kukucurukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.
64 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu yina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.
65 Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.
66 Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzacita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.
67 M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! ndi madzulo mudzati, Mwenzi utafika m'mawa! cifukwa ca mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi cifukwa ca zopenya maso anu zimene mudzazipenya.
68 Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Aigupto ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogulainu.