Deuteronomo 25 BL92

Za makwapulidwe a wolakwa

1 Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.

2 Ndipo kudzali, wocita coipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pace, amwerengere zofikira coipa cace.

3 Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.

4 Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu.

Za kukwatibwa mkazi ndi mlamu wace

5 Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wafayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wace alowane naye, namtenge akhale mkazi wace, namcitire zoyenera mbale wa mwamuna wace.

6 Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lace la mbale wace wafayo, kuti dzina lace lisafafanizidwe m'Israyeli.

7 Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wace, mkazi wa mbale waceyo azikwera kumka kucipata, kwa akuru, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wace dzina m'Israyeli; safuna kundicitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.

8 Pamenepo akuru a mudzi wace amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;

9 pamenepo mkazi wa mbale wace azimyandikiza pamaso pa akuru, nacotse nsapato yace ku ph zi la mwamunayo, ndi kumthira malobvu pankhope pace, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wace.

10 Ndipo azimucha dzina lace m'Israyeli, Nyumba ya uje anamcotsa nsapato.

11 Akalimbana wina ndi mnzace, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wace m'dzanja la wompandayo, nakaturutsa dzanja lace, ndi kumgwira kudzibvalo;

12 pamenepo muzidula dzanja lace; diso lanu lisamcitire cifundo.

13 Musamakhala nayo m'thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukuru ndi waung'ono.

14 Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukuru ndi waung'ono.

15 Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

16 Pakuti onse akucita zinthu izi, onse akucita cisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

Amaleki afafanizike

17 Kumbukilani cocitira inu Amaleki panjira, poturuka inu m'Aigupto;

18 kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofok a akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaopa Mulungu,

19 Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu, kuti muzifafaniza cikumbutso ca Amaleki pansi pa thambo; musamaiwala.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34