Deuteronomo 2 BL92

1 Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kumka kucipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.

2 Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

3 Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kumka kumpoto,

4 Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzyola malire a abale anu, ana a Bsau okhala m'Seiri; ndipo adzakuopani; mucenjere ndithu;

5 musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai pakuti ndapatsa Bsau phiri la Seiri likhale lace lace.

6 Mugulane nao cakudya ndi ndarama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe.

7 Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu nchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'cipululu ici cacikuru; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu.

8 Potero tinapitirira abale athu, ana a Bsau okhala m'Seiri, njira ya cidikha, ku Elati ndi ku Ezioni Geberi.

9 Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya cipululu ca Moabu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usabvuta Moabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lace likhale lako lako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale lao lao.

10 (Aemi anakhalamo kale, ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, ngati Aanaki.

11 Anawayesa iwonso Arefai, monga Aanaki; koma Amoabu awacha Aemi.

12 Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israyeli anacitira dziko lace lace, limene Yehova anampatsa.)

13 Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.

14 Ndipo masiku amene tinayenda kucokera ku Kadesi Barinea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'cigono, monga Yehova adawalumbirira.

15 Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'cigono, kufikira adawatha.

16 Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,

17 Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

18 Lero lomwe utumphe malire a Moabu, ndiwo Ari.

19 Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawabvuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lako lako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale lao lao.

20 (Ilinso aliyesa dziko la Arefai; Arefai anakhalamo kale; koma Aamoni awacha Azamzumi;

21 ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;

22 monga iye anacitira ana a Bsau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe.

23 Kunena za Aavi akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao.)

24 Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, M-amori, ndi dziko lace m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.

25 Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kucititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa cifukwa ca iwe.

26 Ndipo ndinatuma amithenga ocokera ku cipululu ca Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,

27 Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,

28 Undigulitse cakudya ndi ndarama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndarama, kuti ndimwe; cokhaci ndipitire coyenda pansi;

29 monga anandicitira ana a Esau akukhala m'Seiri, ndi Amoabu akukhala m'Ari; kufikira nditaoloka Yordano kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilola kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wace, nalimbitsa mtima wace, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.

31 Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lace pamaso pako; yamba kulandira dziko lace likhale lako lako.

32 Pamenepo Sihoni anaturuka kukomana nafe, iye ndi anthu ace onse, kugwirana nafe nkhondo ku Yahaza.

33 Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ace amuna ndi anthu ace onse.

34 Ndipo muja tinalanda midzi yace yonse; ndipo tinaononga konse midzi yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense.

35 Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za midzi tidailanda.

36 Kuyambira ku Aroeri, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi ku mudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Gileadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ace; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.

37 Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kuli konse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34