1 Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani cizindikilo kapena cozizwa;
2 ndipo cizindikilo kapena cozizwa adanenaci cifika, ndi kuti, Titsate milungu yina, imene simunaidziwa, ndi kuitumikira;
3 musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
4 Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ace, ndi kumvera mau ace, ndi kumtumikira iye, ndi kummamatira.
5 Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena cosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, nakuombolani m'nyumba ya akapolo; kuti akuceteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzicotsa coipaco pakati pa inu.