6 Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanu wanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu yina, imene simunaidziwa, inu, kapena makolo anu;
7 ndiyo milungu ya mitundu ya anthu akuzungulira inu, akukhala pafupi pali inu, kapena akukhala patali pali inu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero ena a dziko lapansi;
8 musamabvomerezana naye, kapena kumvera iye; diso lanu lisamcitire cifundo, kapena kumleka, kapena kumbisa;
9 koma muzimupha ndithu; liyambe dzanja lanu kukhala pa iye kumupha, ndi pamenepo dzanja la anthu onse.
10 Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukucetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba va akapolo.
11 Kuti Israyeli wonse amve, ndi kuopa, ndi kusaonieza kucita coipa cotere conga ici pakati pa inu.
12 Ukamva za umodzi wa midzi yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti,