11 Popeza waumphawi salekana m'dziko, cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.
12 Mukagula mbale wanu, Mhebri wamwamuna kapena Mhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi cimodzi; koma caka cacisanu ndi ciwiri umlole acoke kwanu waufulu.
13 Ndipo pomlola iwe acoke kwanu waufulu, musamamlola acoke wopanda kanthu;
14 mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za padwale, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.
15 Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.
16 Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituruka kucoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;
17 pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwace, kulikanikiza ndi citseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzicitanso momwemo ndi adzakazi anu.