12 Mukagula mbale wanu, Mhebri wamwamuna kapena Mhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi cimodzi; koma caka cacisanu ndi ciwiri umlole acoke kwanu waufulu.
13 Ndipo pomlola iwe acoke kwanu waufulu, musamamlola acoke wopanda kanthu;
14 mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za padwale, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.
15 Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.
16 Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituruka kucoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;
17 pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwace, kulikanikiza ndi citseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzicitanso momwemo ndi adzakazi anu.
18 Musamayesa neosautsa, pomlola akucokereni waufulu; popeza anakugwirirani nchito zaka zisanu ndi cimodzi monga wolipidwa wakulandira cowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzicita.