9 Dzicenjerani, mungakhale mau opanda pace mumtima mwanu, ndi kuti, Cayandika caka cacisanu ndi ciwiri, caka ca cilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale cimo.
10 Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, cifukwa ca ici Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu nchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.
11 Popeza waumphawi salekana m'dziko, cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.
12 Mukagula mbale wanu, Mhebri wamwamuna kapena Mhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi cimodzi; koma caka cacisanu ndi ciwiri umlole acoke kwanu waufulu.
13 Ndipo pomlola iwe acoke kwanu waufulu, musamamlola acoke wopanda kanthu;
14 mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za padwale, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.
15 Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.