6 Mukacipeza cisa ca mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi mace alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga mace pamodzi ndi ana;
7 muloletu mace amuke, koma mudzitengere ana; kuti cikukomereni, ndi kuti masiku anu acuruke.
8 Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lace, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.
9 Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe.
10 Musamalima ndi buru ndi ng'ombe zikoke pamodzi.
11 Musamabvala nsaru yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.
12 Mudzipangire mphonje pa ngondya zinai za copfunda canu cimene mudzipfunda naco.